Beginning
Ku Nyumba ya Wowumba Mbiya
18 Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” 3 Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. 4 Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
5 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 6 “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. 7 Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga, 8 ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira. 9 Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu. 10 Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.
11 “Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’ 12 Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”
13 Yehova akuti,
“Uwafunse anthu a mitundu ina kuti:
Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi?
Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita
chinthu choopsa kwambiri.
14 Kodi chisanu chimatha pa matanthwe
otsetsereka a phiri la Lebanoni?
Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera
ku phiri la Lebanoni adzamphwa?
15 Komatu anthu anga andiyiwala;
akufukiza lubani kwa mafano achabechabe.
Amapunthwa mʼnjira
zawo zakale.
Amayenda mʼnjira zachidule
ndi kusiya njira zabwino.
16 Dziko lawo amalisandutsa chipululu,
chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse;
onse odutsapo adzadabwa kwambiri
ndipo adzapukusa mitu yawo.
17 Ngati mphepo yochokera kummawa,
ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo;
ndidzawafulatira osawathandiza
pa tsiku la mavuto awo.”
18 Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”
19 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;
imvani zimene adani anga akunena za ine!
20 Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?
Komabe iwo andikumbira dzenje.
Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu
kudzawapempherera
kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
21 Choncho langani ana awo ndi njala;
aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga.
Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye;
amuna awo aphedwe ndi mliri,
anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
22 Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo
mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe.
Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo
ndipo atchera msampha mapazi anga.
23 Koma Inu Yehova, mukudziwa
ziwembu zawo zonse zofuna kundipha.
Musawakhululukire zolakwa zawo
kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu.
Agonjetsedwe pamaso panu;
muwalange muli wokwiya.”
19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe 2 ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze. 3 Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. 4 Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. 5 Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. 6 Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu.
7 “ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo. 8 Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake. 9 Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’
10 “Tsono iwe udzaphwanye mtsukowo anthu amene udzapite nawowo akuona, 11 ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. 12 Umu ndi mmene ndidzachitire ndi malo ano pamodzi ndi anthu okhalamo, akutero Yehova. Ndidzasandutsa mzindawu kukhala ngati Tofeti. 13 Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”
14 Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti, 15 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”
Yeremiya ndi Pasuri
20 Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi. 2 Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. 3 Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse. 4 Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo. 5 Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. 6 Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
7 Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;
Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.
Anthu akundinyoza tsiku lonse.
Aliyense akundiseka kosalekeza.
8 Nthawi iliyonse ndikamayankhula,
ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!
Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka
ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
9 Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye
kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”
mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,
amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.
Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,
koma sindingathe kupirirabe.
10 Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,
“Zoopsa ku mbali zonse!
Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”
Onse amene anali abwenzi anga
akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,
“Mwina mwake adzanyengedwa;
tidzamugwira
ndi kulipsira pa iye.”
11 Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.
Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.
Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.
Manyazi awo sadzayiwalika konse.
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama
ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu.
Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga
popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
13 Imbirani Yehova!
Mutamandeni Yehova!
Iye amapulumutsa wosauka
mʼmanja mwa anthu oyipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15 Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga
ndi uthenga woti:
“Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene
Yehova anayiwononga mopanda chisoni.
Amve mfuwu mmawa,
phokoso la nkhondo masana.
17 Chifukwa sanandiphere mʼmimba,
kuti amayi anga asanduke manda anga,
mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18 Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni
kuti moyo wanga
ukhale wamanyazi wokhawokha?
Mulungu Akana Pempho la Zedekiya
21 Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya. 2 Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”
3 Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti, 4 ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. 5 Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali. 6 Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa. 7 Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’
8 “Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. 9 Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. 10 Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.
11 “Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova; 12 inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti,
“ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse;
pulumutsani mʼdzanja la wozunza
aliyense amene walandidwa katundu wake,
kuopa kuti ukali wanga ungabuke
ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika
chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.
13 Ndidzalimbana nanu,
inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa,
inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,
akutero Yehova.
Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe?
Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’
14 Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu,
akutero Yehova.
Ndidzatentha nkhalango zanu;
moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’ ”
Chiweruzo kwa Mafumu Oyipa
22 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, 2 ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. 3 Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. 4 Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. 5 Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”
6 Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:
“Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine,
ngati msonga ya phiri la Lebanoni,
komabe ndidzakusandutsa chipululu,
ngati mizinda yopanda anthu.
7 Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,
munthu aliyense ali ndi zida zake,
ndipo adzadula mikungudza yako yokongola
nadzayiponya pa moto.
8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’ 9 Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”
10 Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;
mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo,
chifukwa sadzabwereranso
kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso. 12 Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”
13 “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,
womanga zipinda zake zosanja monyenga,
pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata,
osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu
ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’
Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu,
ndi kukhomamo matabwa a mkungudza
ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
15 “Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri
zingachititse iwe kukhala mfumu?
Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa.
Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera,
ndipo zonse zinkawayendera bwino.
16 Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,
ndipo zonse zinkamuyendera bwino.
Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?”
akutero Yehova.
17 “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,
koma zili pa phindu lachinyengo,
pa zopha anthu osalakwa
ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,
“Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti,
‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!
Anthu ake sadzamulira maliro kuti,
Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
19 Adzayikidwa ngati bulu,
kuchita kumuguguza ndi kukamutaya
kunja kwa zipata za Yerusalemu.”
20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,
mawu anu akamveke mpaka ku Basani.
Mulire mofuwula muli ku Abarimu
chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.
Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’
Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono.
Simunandimvere Ine.
22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,
ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo.
Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa
chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,
amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza,
mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani,
zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!
24 “Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya. 25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. 26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. 27 Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”
28 Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,
yosweka imene anthu sakuyifunanso?
Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake,
achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
29 Iwe dziko, dziko, dziko,
Imva mawu a Yehova!
30 Yehova akuti,
“Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana,
munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse,
pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino.
Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide
ndi kulamulira Yuda.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.