Beginning
Uthenga Wonena za Aamoni
49 Yehova ananena izi:
Amoni,
“Kodi Israeli alibe ana aamuna?
Kapena alibe mlowamʼmalo?
Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?
Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
2 Koma nthawi ikubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo
ku Raba, likulu la Amoni;
ndipo malo awo opembedzera milungu yawo
adzatenthedwa ndi moto.
Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo
kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”
akutero Yehova.
3 “Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!
Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!
Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;
thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,
chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
4 Chifukwa chiyani mukunyadira
chigwa chanu,
inu anthu osakhulupirika
amene munadalira chuma chanu nʼkumati:
‘Ndani angandithire nkhondo?’
5 Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe
zochokera kwa onse amene akuzungulira,”
akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.
“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.
Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.
6 “Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”
akutero Yehova.
Uthenga Wonena za Edomu
7 Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:
“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?
Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?
Kodi nzeru zawo zinatheratu?
8 Inu anthu a ku Dedani, thawani,
bwererani ndi kukabisala ku makwalala
chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau
popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
9 Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu
akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Anthu akuba akanafika usiku
akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
10 Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.
Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,
kotero kuti sadzathanso kubisala.
Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.
Palibe wonena kuti,
11 ‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.
Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”
12 Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. 13 Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:
Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,
“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!
Konzekerani nkhondo!”
15 “Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.
Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
16 Kuopseza kwako kwakunyenga;
kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga
a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.
Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,
ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
akutero Yehova.
17 “Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.
Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo
chifukwa cha kuwonongeka kwake.
18 Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,
pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”
akutero Yehova,
“motero palibe munthu
amene adzakhala mu Edomu.
19 “Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani
kupita ku malo a msipu wobiriwira,
Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.
Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.
Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?
Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
20 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova
ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
21 Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;
kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22 Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka
nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu
idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Uthenga Wonena za Damasiko
23 Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:
“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha
chifukwa amva nkhani yoyipa.
Mitima yawo yagwidwa ndi mantha
ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
24 Anthu a ku Damasiko alefuka.
Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa
chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.
Ali ndi nkhawa komanso mantha
ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
25 Mzinda wotchuka
ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
26 Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;
ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
27 “Ndidzatentha malinga a Damasiko;
moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
Uthenga Wonena za Kedara ndi Hazori
28 Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:
“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.
Kawonongeni anthu a kummawako.
29 Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,
ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.
Mutengenso ngamira zawo.
Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,
‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
30 “Thawani mofulumira!
Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”
akutero Yehova.
“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;
wakonzekera zoti alimbane nanu.
31 “Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,
umene ukukhala mosatekeseka,”
akutero Yehova,
“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;
anthu ake amakhala pa okha.
32 Ngamira zawo zidzafunkhidwa,
ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.
Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.
Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”
akutero Yehova.
33 “Hazori adzasanduka bwinja,
malo okhalamo nkhandwe
mpaka muyaya.
Palibe munthu amene adzayendemo.”
Uthenga Wonena za Elamu
34 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:
35 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,
umene uli chida chawo champhamvu.
36 Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu
kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;
ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,
ndipo sipadzakhala dziko
limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
37 A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo
komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.
Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga
ndipo adzakhala pa mavuto,”
akutero Yehova.
“Ndidzawapirikitsa ndi lupanga
mpaka nditawatheratu.
38 Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu
ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”
akutero Yehova.
39 “Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera
anthu a ku Elamu dziko lawo,”
akutero Yehova.
Uthenga Wonena za Babuloni
50 Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu:
2 “Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina,
kweza mbendera ndipo ulengeze;
usabise kanthu, koma uwawuze kuti,
‘Babuloni wagwa;
mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi,
nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha.
Milungu yake yagwidwa ndi mantha
ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’
3 Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni
ndi kusandutsa bwinja dziko lake.
Kumeneko sikudzakhalanso
munthu kapena nyama.
4 “Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”
akutero Yehova,
“anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda
onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.
5 Adzafunsa njira ya ku Ziyoni
ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko.
Iwo adzadzipereka kwa Yehova
pochita naye pangano lamuyaya
limene silidzayiwalika.
6 “Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika;
abusa awo
anawasocheretsa mʼmapiri.
Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda
mpaka kuyiwala kwawo.
7 Aliyense amene anawapeza anawawononga;
adani awo anati, ‘Ife si olakwa,
chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniweni
ndi amene makolo awo anamukhulupirira.’
8 “Thawaniko ku Babuloni;
chokani mʼdziko la Ababuloni.
Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto.
9 Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina
ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto
kudzamenyana ndi Babuloni.
Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni.
Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso,
yosapita padera.
10 Motero Ababuloni adzafunkhidwa;
ndipo onse omufunkha adzakhuta,”
akutero Yehova.
11 “Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika.
Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala.
Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu
ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.
12 Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri.
Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa.
Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse.
Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.
13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu
ndipo adzakhala chipululu chokhachokha.
Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya
chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.
14 “Inu okoka uta,
konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse.
Muponyereni mivi yanu yonse
chifukwa anachimwira Yehova.
15 Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja.
Nsanja zake zagwa.
Malinga ake agwetsedwa.
Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova.
Mulipsireni,
mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.
16 Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense,
ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola.
Poona lupanga la ozunza anzawo,
aliyense adzabwerera kwa anthu ake;
adzathawira ku dziko la kwawo.
17 “Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika
pothamangitsidwa ndi mikango.
Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo.
Wotsiriza anali Nebukadinezara
mfumu ya ku Babuloni
amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”
18 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake
monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.
19 Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake
ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani;
adzadya nakhuta ku mapiri
a ku Efereimu ndi Giliyadi.
20 Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”
akutero Yehova,
“anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli
koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe,
ndipo adzafufuza machimo a Yuda,
koma sadzapeza ndi limodzi lomwe,
chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.
21 “Lithireni nkhondo dziko la Merataimu
ndi anthu okhala ku Pekodi.
Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,”
akutero Yehova.
“Chitani zonse monga momwe ndakulamulani.
22 Mʼdziko muli phokoso la nkhondo,
phokoso la chiwonongeko chachikulu!
23 Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera
uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi.
Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha
pakati pa mitundu ina!
24 Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni,
ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu;
unapezeka ndiponso unakodwa
chifukwa unalimbana ndi Yehova.
25 Yehova watsekula nyumba ya zida zake
ndipo watulutsa zida za ukali wake,
pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire
mʼdziko la Ababuloni.
26 Mumenyane naye Babuloni mbali zonse.
Anthu ake muwawunjike
ngati milu ya tirigu.
Muwawononge kotheratu
ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
27 Iphani ankhondo ake onse.
Onse aphedwe ndithu.
Tsoka lawagwera
pakuti tsiku lawo lachilango lafika.
28 Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloni
akulengeza mu Yerusalemu
za kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu.
Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake.
29 “Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni.
Muyitanenso onse amene amakoka mauta.
Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira;
musalole munthu aliyense kuthawa.
Muchiteni monga momwe
iye anachitira anthu ena.
Iyeyu ananyoza
Yehova, Woyera wa Israeli.
30 Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake;
ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,”
akutero Yehova.
31 “Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,”
akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,
“chifukwa tsiku lako lafika,
nthawi yoti ndikulange yakwana.
32 Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwa
ndipo palibe amene adzakudzutse;
ndidzayatsa moto mʼmizinda yake
umene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.”
33 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Anthu a ku Israeli akuzunzidwa,
pamodzi ndi anthu a ku Yuda,
ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa,
akukana kuwamasula.
34 Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo
nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo,
koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”
35 Yehova akuti,
“Imfa yalunjika pa Ababuloni,
pa akuluakulu ake
ndi pa anthu ake a nzeru!
36 Imfa yalunjika pa aneneri abodza
kuti asanduke zitsiru.
Imfa yalunjika pa ankhondo ake
kuti agwidwe ndi mantha aakulu.
37 Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake.
Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo
kuti asanduke ngati akazi.
Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake
kuti chidzafunkhidwe.
38 Chilala chilunjike pa madzi ake
kuti aphwe.
Babuloni ndi dziko la mafano,
ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.
39 “Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko
ndipo kudzakhalanso akadzidzi.
Kumeneko sikudzapezekako anthu,
ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.
40 Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora
pamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,”
akutero Yehova,
“momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko;
anthu sadzayendanso mʼmenemo.
41 “Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri,
wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
42 Atenga mauta ndi mikondo;
ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo.
Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo awo,
ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo
iwe Babuloni.
43 Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo,
ndipo yalobodokeratu.
Ikuda nkhawa,
ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.
44 Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani
kupita ku msipu wobiriwira,
momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi.
Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine.
Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane?
Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”
45 Nʼchifukwa chake imvani.
Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
46 Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera,
ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.