Beginning
Tsoka kwa Amene Amadalira Igupto
31 Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,
amene amadalira akavalo,
nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo
ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,
koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,
kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,
ndipo sasintha chimene wanena.
Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,
komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu;
akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu.
Yehova akangotambasula dzanja lake,
amene amapereka chithandizo adzapunthwa,
amene amalandira chithandizocho adzagwa;
onsewo adzathera limodzi.
4 Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi:
“Monga mkango kapena msona wamkango umabangula
ukagwira nyama yake,
ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka
ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,
momwemonso palibe chingaletse
Yehova Wamphamvuzonse
kubwera kudzatchinjiriza
phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,
Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;
ndi kumupulumutsa,
iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu. 7 Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 “Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.
Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.
Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo
adzagwira ntchito yathangata.
9 Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,
ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha
kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”
Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,
ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
Ufumu Wachilungamo
32 Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,
ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
2 Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo
ndi malo obisalirapo namondwe,
adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,
ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
3 Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
4 Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,
ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
5 Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake
ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
6 Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,
amaganiza kuchita zoyipa:
Iye amachita zoyipira Mulungu,
ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;
anjala sawapatsa chakudya
ndipo aludzu sawapatsa madzi.
7 Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,
iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.
Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake
ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
8 Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,
Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
Akazi a ku Yerusalemu
9 Khalani maso, inu akazi
amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji
ndipo imvani mawu anga.
Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 Pakapita chaka ndi masiku pangʼono
inu akazi amatama mudzanjenjemera;
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika
ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;
ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.
Vulani zovala zanu,
ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,
ndi mphesa yawonongeka.
13 Mʼdziko la anthu anga
mwamera minga ndi mkandankhuku.
Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero
ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;
malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.
Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 Yehova adzatipatsa mzimu wake,
ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,
ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama
ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;
zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,
mʼnyumba zodalirika,
ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala
ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 inutu mudzakhala odalitsika ndithu.
Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,
ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
Msautso ndi Thandizo
33 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,
amene sunawonongedwepo!
Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,
iwe amene sunanyengedwepo!
Iwe ukadzaleka kuwononga,
udzawonongedwa,
ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,
ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
2 Inu Yehova, mutikomere mtima ife;
tikulakalaka Inu.
Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,
ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
3 Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;
pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
4 Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.
Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
5 Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse
adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
6 Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,
adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;
kuopa Yehova ngati madalitso.
7 Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;
akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
8 Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,
mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.
Mdaniyo ndi wosasunga pangano.
Iye amanyoza mboni.
Palibe kulemekezana.
9 Dziko likulira ndipo likunka likutha.
Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.
Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.
Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka
ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,
ndipo ndidzakwezedwa.
11 Zolingalira zanu nʼzachabechabe
ngati udzu wamanyowa.
Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;
ndi ngati minga yodulidwa.”
13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;
inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;
anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:
Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?
Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungama
ndi kuyankhula zoona,
amene amakana phindu lolipeza monyenga
ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,
amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo
ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,
kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.
Azidzalandira chakudya chake
ndipo madzi sadzamusowa.
17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
“Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
chachilendo ndi chosamveka.
20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
maso anu adzaona Yerusalemu,
mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
kapena zingwe zake kuduka.
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,
sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,
matanga ake sakutheka kutambasuka.
Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri
ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”
ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
Chiweruzo cha Anthu a Mitundu Yonse
34 Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve:
tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse:
Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
2 Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse;
wapsera mtima magulu awo onse ankhondo.
Iye adzawawononga kotheratu,
nawapereka kuti aphedwe.
3 Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja,
mitembo yawo idzawola ndi kununkha;
mapiri adzafiira ndi magazi awo.
4 Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka
ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala;
nyenyezi zonse zidzayoyoka
ngati masamba ofota a mphesa,
ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
5 Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba;
taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu,
anthu amene ndawawononga kotheratu.”
6 Lupanga la Yehova lakhuta magazi,
lakutidwa ndi mafuta;
magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi,
mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna.
Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira
ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
7 Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati,
ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe.
Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,
ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
8 Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira
ndi kulanga adani a Ziyoni.
9 Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula,
ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule;
dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
10 Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana;
utsi wake udzafuka kosalekeza.
Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado;
palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
11 Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu;
amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo.
Mulungu adzatambalitsa pa Edomu
chingwe choyezera cha chisokonezo
ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
12 Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko;
akalonga ake onse adzachotsedwa.
13 Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa,
khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake.
Ankhandwe azidzadya mʼmenemo;
malo okhalamo akadzidzi.
14 Avumbwe adzakumana ndi afisi,
ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana.
Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa
ndi kupeza malo opumulirako.
15 Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira,
adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake;
akamtema adzasonkhananso kumeneko,
awiriawiri.
16 Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga:
mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa;
sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake.
Pakuti Yehova walamula kuti zitero,
ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
17 Yehova wagawa dziko lawo;
wapatsa chilichonse chigawo chake.
Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya
ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.
Chimwemwe cha Opulumutsidwa
35 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;
dziko lowuma lidzakondwa
ndi kuchita maluwa. 2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka
lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.
Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.
Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova,
ukulu wa Mulungu wathu.
3 Limbitsani manja ofowoka,
limbitsani mawondo agwedegwede;
4 nenani kwa a mitima yamantha kuti;
“Limbani mtima, musachite mantha;
Mulungu wanu akubwera,
akubwera kudzalipsira;
ndi kudzabwezera chilango adani anu;
akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso
ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala,
ndipo osayankhula adzayimba mokondwera.
Akasupe adzatumphuka mʼchipululu
ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe,
nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe.
Pamene panali mbuto ya ankhandwe
padzamera udzu ndi bango.
8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu;
ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika.
Anthu odetsedwa
sadzayendamo mʼmenemo;
zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 Kumeneko sikudzakhala mkango,
ngakhale nyama yolusa sidzafikako;
sidzapezeka konse kumeneko.
Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.
Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;
kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.
Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,
ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.