Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 63:7-9

Matamando ndi Pemphero

Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,
    ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.
    Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.
Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake
    Yehova wachitira nyumba ya Israeli
    zinthu zabwino zambiri.
Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,
    ana anga amene sadzandinyenga Ine.”
    Choncho anawapulumutsa.
Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,
    ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.
Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,
    anawanyamula ndikuwatenga
    kuyambira kale lomwe.

Masalimo 148

148 Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
    mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
Mutamandeni, inu angelo ake onse,
    mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
    mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
    ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
Zonse zitamande dzina la Yehova
    pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
    analamula ndipo sizidzatha.

Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
    inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
    mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
inu mapiri ndi zitunda zonse,
    inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
    inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
    inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
    inu nkhalamba ndi ana omwe.

13 Onsewo atamande dzina la Yehova
    pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
    ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
    matamando a anthu ake onse oyera mtima,
    Aisraeli, anthu a pamtima pake.

Tamandani Yehova.

Ahebri 2:10-18

10 Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. 11 Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake. 12 Iye akuti,

“Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu.
    Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.”

13 Ndiponso,

“Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.”

Ndiponso Iye akuti,

“Ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Mulungu wandipatsa.”

14 Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa. 15 Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. 16 Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu. 17 Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu. 18 Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

Mateyu 2:13-23

Athawira ku Igupto

13 Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.” 14 Atadzuka, Yosefe anatenga mwanayo ndi amayi ake usiku omwewo napita ku Igupto, 15 nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”

Kuphedwa kwa Ana mʼBetelehemu

16 Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza. 17 Pamenepo, zimene ananena mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa:

18 “Kulira kukumveka ku Rama,
    kubuma ndi kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake;
    sakutonthozeka,
chifukwa ana akewo palibe.”

Abwerera ku Nazareti

19 Atamwalira Herode, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto ku Igupto 20 nanena kuti, “Nyamuka, tenga mwanayo ndi amayi ake ndipo mupite ku dziko la Israeli, popeza amene anafuna moyo wa mwanayo anamwalira.”

21 Tsono Yosefe atadzuka anatenga mwanayo ndi amayi ake kupita ku dziko la Israeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao akulamulira mu Yudeya mʼmalo mwa abambo ake, Herode, anaopa kupitako. Atachenjezedwa mʼmaloto, anapita ku Galileya, 23 ndipo anakakhazikika mu mzinda wa Nazareti. Pamenepo zinakwaniritsidwa zonenedwa ndi aneneri kuti, “Adzatchedwa Mnazareti.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.