); Proverbs 8:22-31 (Wisdom’s part in creation); 1 John 5:1-12 (Whoever loves God loves God’s child) (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
148 Tamandani Yehova.
Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse,
mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
5 Zonse zitamande dzina la Yehova
pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
analamula ndipo sizidzatha.
7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
9 inu mapiri ndi zitunda zonse,
inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
inu nkhalamba ndi ana omwe.
13 Onsewo atamande dzina la Yehova
pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
matamando a anthu ake onse oyera mtima,
Aisraeli, anthu a pamtima pake.
Tamandani Yehova.
22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.
Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 Ndinapangidwa kalekalelo,
pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,
zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,
mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;
lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,
pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga
ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 pamene anayikira nyanja malire
kuti madzi asadutse malirewo,
ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30 Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;
ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,
kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse
ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
Chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu
5 Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake. 2 Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake. 3 Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, 4 chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. 5 Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
6 Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi. 7 Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. 8 Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana. 9 Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. 10 Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. 11 Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. 12 Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.