Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 42

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
    kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
    Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
Misozi yanga yakhala chakudya changa
    usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”
Zinthu izi ndimazikumbukira
    pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
    kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
    pakati pa anthu a pa chikondwerero.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
    pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi     Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
    kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
    ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
Madzi akuya akuyitana madzi akuya
    mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
    andimiza.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
    nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
    pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
    “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
    pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”

11 Bwanji ukumva chisoni,
    iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
    Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
    Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Ezekieli 47:1-12

Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu

47 Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.

Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”

Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10 Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11 Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12 Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”

Yuda 17-25

Awalimbikitsa kuti Apirire

17 Koma okondedwa, kumbukirani zimene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu ananeneratu. 18 Iwo anakuwuzani kuti, “Mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsatira zofuna zawo zoyipa.” 19 Anthu amenewa ndi amene akubweretsa mipatuko pakati panu, amatsatira nzeru zachibadwa ndipo alibe Mzimu Woyera.

20 Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. 21 Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.

22 Muwachitire chifundo amene akukayika. 23 Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.

Mawu Olemekeza Mulungu

24 Kwa Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe mʼmachimo, ndiponso amene angathenso kukufikitsani pamaso pake pa ulemerero wopanda cholakwa muli okondwa, 25 kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.