Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 97

97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
    magombe akutali akondwere.

Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
    chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Moto umapita patsogolo pake
    ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
    pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
    ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
    iwo amene amanyadira mafano;
    mulambireni, inu milungu yonse!

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
    midzi ya Yuda ikusangalala
    chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
    ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
    pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
    ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
    ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
    ndipo tamandani dzina lake loyera.

Eksodo 33:18-23

18 Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.”

19 Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” 20 Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.”

21 Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. 22 Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.”

Yohane 1:14-18

14 Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.

15 Yohane achitira umboni za Iye. Iye akufuwula kuti, “Uyu ndi Iye amene ndinati, ‘Iye amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa, Iyeyo analipo ine ndisanabadwe.’ ” 16 Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso. 17 Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu. 18 Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.