Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 121

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
    kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Sadzalola kuti phazi lako literereke;
    Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
    sadzawodzera kapena kugona.

Yehova ndiye amene amakusunga;
    Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
    kapena mwezi nthawi ya usiku.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
    adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Ezekieli 1:26-2:1

26 Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu. 27 Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo. 28 Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula.

Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.

Kuyitanidwa kwa Ezekieli

Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.”

Machitidwe a Atumwi 26:1-18

Mawu a Paulo Pamaso pa Mfumu Agripa

26 Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti, “Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera, ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.

“Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu. Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa. Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu. Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu. Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?

“Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10 Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza. 11 Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.

12 “Pa ulendo wina wotere, ndikupita ku Damasiko ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa akulu a ansembe, 13 Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo. 14 Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ”

15 Ndipo ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?”

Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza. 16 Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa. 17 Ine ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu a mtundu wako ndiponso mwa anthu a mitundu ina. Ine ndikukutuma kwa iwo, 18 kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.