Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 97

97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
    magombe akutali akondwere.

Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
    chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Moto umapita patsogolo pake
    ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
    pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
    ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
    iwo amene amanyadira mafano;
    mulambireni, inu milungu yonse!

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
    midzi ya Yuda ikusangalala
    chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
    ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
    pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
    ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
    ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
    ndipo tamandani dzina lake loyera.

Eksodo 33:12-17

Mose ndi Ulemerero wa Yehova

12 Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ 13 Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”

14 Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”

15 Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. 16 Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”

17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.”

Chivumbulutso 22:6-9

Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”

Yesu Akubweranso

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”

Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.