Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 67

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.

67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
    achititse kuti nkhope yake itiwalire.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
    chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
    pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
    ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

Nthaka yabereka zokolola zake;
    tidalitseni Mulungu wathu.
Mulungu atidalitse
    kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Miyambo 2:9-15

Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,
    kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako,
    kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga;
    kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.

12 Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa,
    kwa anthu amabodza,
13 amene amasiya njira zolungama
    namayenda mʼnjira zamdima,
14 amene amakondwera pochita zoyipa
    namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota,
    ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.

Luka 19:1-10

Zakeyu Apulumutsidwa

19 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”

Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10 Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.