Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 9:1-6

Kutembenuka Mtima kwa Saulo

Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe, ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu. Akuyandikira ku Damasikoku paulendo wake, mwadzidzidzi kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira iye. Iye anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti, “Saulo, Saulo ukundizunziranji Ine?”

Saulo anafunsa kuti, “Ndinu yani Ambuye?”

Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.” “Tsopano dzuka, lowa mu mzindamo, ndipo udzawuzidwa zoyenera kuchita.”

Machitidwe a Atumwi 9:7-20

Anthu amene anali naye paulendo, anasowa chonena; iwo anamva mawu koma sanaone wina aliyense. Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko. Anakhala wosaona kwa masiku atatu ndiponso sanadye kapena kumwa kanthu kalikonse.

10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!”

Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.”

11 Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera. 12 Ndipo waona mʼmasomphenya munthu, dzina lake Hananiya atabwera ndi kumusanjika manja kuti aonenso.”

13 Hananiya anayankha kuti, “Ambuye, ndinamva zambiri za munthu uyu ndi zonse zoyipa anachitira oyera mtima a ku Yerusalemu. 14 Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu ansembe kuti adzamange onse amene amayitana pa dzina lanu.”

15 Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli. 16 Ine ndidzamuonetsa zowawa zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.”

17 Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.” 18 Nthawi yomweyo mʼmaso mwa Saulo munachoka zinthu zokhala ngati mamba ansomba, ndipo anayambanso kuona. Iye anayimirira nabatizidwa, 19 ndipo atadya chakudya, anapezanso mphamvu.

Saulo Alalikira ku Damasiko

Saulo anakhala masiku angapo ndi ophunzira a ku Damasiko. 20 Posakhalitsa anayamba kulalikira mʼsunagoge kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu.

Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Chivumbulutso 5:11-14

11 Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. 12 Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti,

“Mwana Wankhosa amene anaphedwayu
    ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu,
    ulemerero ndi mayamiko.”

13 Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,

“Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,
    kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu
mpaka muyaya!”

14 Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.

Yohane 21:1-19

Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya

21 Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.

Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.

Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?”

Iwo anayankha kuti, “Ayi.”

Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.

Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.

10 Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”

11 Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike. 12 Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye. 13 Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba. 14 Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.

Yesu Abwezeretsa Petro

15 Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?”

Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”

16 Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”

Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”

17 Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”

Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”

Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga. 18 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” 19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.