Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4 Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5 Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
25 “ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”
29 Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. 30 Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. 31 Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.
Chuma cha Kumwamba
32 “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.