Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 16:9-15

Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.” 10 Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.

Lidia Atembenuka Mtima ku Filipi

11 Kuchokera ku Trowa tinakwera sitima ya pamadzi kupita ku Samotrake ndipo mmawa mwake tinapitirira mpaka ku Neapoli. 12 Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.

13 Pa tsiku la Sabata tinatuluka mu mzindawo kupita ku mtsinje kumene timayembekezera kukapeza malo opempherera. Tinakhala pansi ndipo tinayamba kuyankhula ndi amayi amene anasonkhana pamenepo. 14 Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo. 15 Iye ndi a mʼbanja lake atabatizidwa, anatiyitana kuti tipite ku nyumba yake. Iye anati, “Ngati mwanditenga ine kukhala wokhulupirira mwa Ambuye, bwerani mudzakhale mʼnyumba mwanga.” Ndipo anatiwumiriza ife kwambiri.

Masalimo 67

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.

67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
    achititse kuti nkhope yake itiwalire.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
    chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
    pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
    ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

Nthaka yabereka zokolola zake;
    tidalitseni Mulungu wathu.
Mulungu atidalitse
    kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Chivumbulutso 21:10

10 Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.

Chivumbulutso 21:22-22:5

22 Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake. 23 Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja. 24 Mitundu ya anthu idzayenda mʼkuwala kwake ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mu mzindamo. 25 Zipata zake sizidzatsekedwa ngakhale tsiku limodzi lomwe pakuti sikudzakhala usiku kumeneko. 26 Ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu adzapita nazo kumeneko. 27 Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.

Mtsinje Wamoyo

22 Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa, Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina. Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

Yohane 14:23-29

23 Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24 Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

25 “Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27 Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29 Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire.

Yohane 5:1-9

Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata

Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”

Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”

Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.

Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.