Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 25:1-10

Salimo la Davide.

25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
    Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
    kapena kuti adani anga andipambane.
Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
    sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
    ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
    phunzitseni mayendedwe anu;
tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
    pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
    ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
    pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
    ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
    pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
    choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
    ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
    kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.

Nehemiya 9:16-25

16 “Koma makolo athu anadzikuza ndi kuwumitsa khosi, ndipo iwo sanamvere malamulo anu. 17 Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye. 18 Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa.

19 “Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku. 20 Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa. 21 Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”

22 “Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo. 23 Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga. 24 Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire. 25 Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana.

1 Atesalonika 5:12-22

Malangizo Otsiriza

12 Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. 13 Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. 14 Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.

16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20 Musanyoze mawu a uneneri. 21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.