Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Naomi ndi Rute
1 Mu nthawi imene oweruza ankalamulira Israeli, munali njala mʼdziko, ndipo munthu wina wa ku Betelehemu mʼdziko la Yuda anapita pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna awiri, kukakhala ku Mowabu kwa nthawi yochepa. 2 Dzina la munthuyo linali Elimeleki, dzina la mkazi wake linali Naomi, ndipo mayina a ana awo aamuna anali Maaloni ndi Kiliyoni. Iwo anali Aefurati ochokera ku Betelehemu ku Yuda. Ndipo anapita kukakhala ku Mowabu.
3 Kenaka Elimeleki, mwamuna wake wa Naomi anamwalira ndipo Naomiyo anatsala ndi ana ake aamuna awiri aja.
4 Iwo anakwatira akazi a Chimowabu; wina dzina lake Oripa ndi wina Rute. Atakhala kumeneko pafupifupi zaka khumi, 5 Maloni ndi Kiliyoni anamwaliranso kotero kuti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja ndi mwamuna wake.
6 Naomi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kubwerera kwawo kuchokera ku Mowabu popeza anali atamva ali ku Mowabuko kuti Yehova anakomera mtima anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.
7 Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja anachoka kumene ankakhala ndi kuyamba ulendo obwerera kwawo ku Yuda.
8 Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.
9 “Yehova akuthandizeni kuti aliyense wa inu apeze pokhala pabwino komanso mwamuna.” Kenaka anawapsompsona koma awiriwo analira mokweza.
10 Ndipo anati kwa Naomi, “Ife tipita nawo kwa anthu akwanu.”
11 Koma Naomi anati, “Bwererani kwanu ana anga. Chifukwa chiyani mukufuna kupita ndi ine? Kodi ine ndingaberekenso ana ena kuti akhale amuna anu? 12 Bwererani kwanu ana anga muzipita kwanu. Ine ndakalamba kwambiri kotero kuti sindingakwatiwenso. Ngakhale ndikananena kuti ndili nacho chikhulupiriro, ngakhale ndikanakhala ndi mwamuna usiku uno, ndipo nʼkubala ana aamuna, 13 kodi inu mukanadikira kuti akule? Kodi mukanakhalabe osakwatiwa kudikira iwowo? Ayi ana anga. Zimenezi zikundiwawa kwambiri kuposa inu, chifukwa ndi ineyo amene Yehova wafuna kuti ndizunzike.”
14 Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
15 Naomi anati “Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako.”
16 Koma Rute anayankha kuti, “Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. 17 Kumene mukafere inenso ndidzafera komweko ndipo komweko ndikayikidwa mʼmanda. Yehova andichite choyipa chingakule motani, ngati china chingatirekanitse ife kupatula imfa.”
18 Naomi atazindikira kuti Rute watsimikiza kupita naye, analeka kumukakamiza.
146 Tamandani Yehova.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
2 Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.
3 Musamadalire mafumu,
anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.
5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi
Mulungu wa Yakobo.
6 Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
7 Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
8 Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
Yehova amakonda anthu olungama.
9 Yehova amasamalira alendo
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.
Tamandani Yehova.
Magazi a Yesu
11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.
Lamulo Lalikulu Koposa
28 Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”
29 Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31 Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”
32 Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33 Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”
34 Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.