Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Pemphero la Hana
2 Ndipo Hana anapemphera nati,
“Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova;
Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova.
Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola.
Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.
2 “Palibe wina woyera ngati Yehova,
palibe wina koma inu nokha,
palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.
3 “Musandiyankhulenso modzitama,
pakamwa panu pasatuluke zonyada,
pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,
ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.
4 “Mauta a anthu ankhondo athyoka
koma anthu ofowoka avala dzilimbe.
5 Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya,
koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala.
Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri,
koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.
6 “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo,
amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.
7 Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa,
amatsitsa ndipo amakweza.
8 Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi,
ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala.
Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu,
amawapatsa mpando waulemu.
“Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova,
anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
9 Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika
koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima.
“Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.
10 Yehova adzaphwanya omutsutsa.
Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba;
Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi.
“Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,
adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”
18 Koma Samueli amatumikira pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala. 19 Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka. 20 Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.” 21 Ndipo Yehova anamukomera mtima Hana. Anakhala ndi pathupi ndi kubereka ana aamuna atatu ndi ana aakazi awiri. Ndipo Samueli ankakula pamaso pa Yehova.
Za Moyo Weniweni mwa Khristu
6 Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. 7 Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
8 Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
9 Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. 10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. 11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. 12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. 14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. 15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.