Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 18:20-30

20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
    molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
    ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
    sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
    ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
    molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.

25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
    kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
    koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
    koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
    Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
    ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
    mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
    kwa onse amene amathawira kwa Iye.

Rute 2:15-23

15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi. 16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”

17 Choncho Rute anakunkha mʼmundamo mpaka madzulo. Kenaka anapuntha barele anakunkhayo, ndipo anakwanira pafupifupi makilogalamu khumi.

18 Anasenza barele uja kupita naye ku mudzi, nakaonetsa apongozi ake. Kenaka anatulutsa chakudya chimene chinatsalira atakhuta chija ndi kupatsa apongozi ake.

19 Apongozi akewo anamufunsa kuti, “Kodi lero unakakunkha kuti? Unakagwira kuti ntchitoyi? Adalitsike munthu amene anakukomera mtimayo.” Ndipo Rute anawuza mpongozi wake za munthu amene ku malo ake anakagwirako ntchito. Iye anati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.”

20 Naomi anati kwa mpongozi wakeyo, “Munthu ameneyu amudalitse Yehova, amene sanasiye kuchitira chifundo anthu amoyo ndi akufa omwe. Anatinso munthu ameneyu ndi mnansi wapaphata. Ndiye ali ndi udindo wotisamalira.”

21 Choncho Rute Mmowabuyo anati, “Iye anandiwuzanso kuti, ‘Uzitsata antchito angawa mpaka atamaliza kukolola munda wonse.’ ”

22 Naomi anati kwa Rute mpongozi wake, “Kuli bwino mwana wanga kuti uzipita ndi adzakazi ake kuopa kuti mʼmunda wa munthu wina angakuvute.”

23 Choncho Rute ankatsatira adzakazi a Bowazi namakunkha mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Ndipo amakhalabe ndi mpongozi wakeyo.

Aroma 12:17-21

17 Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense. 18 Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere. 19 Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. 20 Koma,

“Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya.
    Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa.
Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”

21 Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.

Aroma 13:8-10

Chikondi Chimakwaniritsa Malamulo

Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 10 Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.