Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
ndi mavuto onse anapirira.
2 Iye analumbira kwa Yehova
ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
3 “Sindidzalowa mʼnyumba mwanga
kapena kugona pa bedi langa:
4 sindidzalola kuti maso anga agone,
kapena zikope zanga ziwodzere,
5 mpaka nditamupezera malo Yehova,
malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
6 Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata,
tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
7 “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo;
tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
8 ‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira,
Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
9 Ansembe anu avekedwe chilungamo;
anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”
10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu,
musakane wodzozedwa wanu.
11 Yehova analumbira kwa Davide,
lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha:
“Mmodzi wa ana ako
ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12 ngati ana ako azisunga pangano langa
ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa,
pamenepo ana awo adzakhala pa mpando
wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
13 Pakuti Yehova wasankha Ziyoni,
Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14 “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi;
ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15 Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri;
anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16 Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso,
ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
17 “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18 Ndidzaveka adani ake manyazi,
koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
Yosiya Akonzanso Pangano
23 Pamenepo mfumu inayitanitsa akuluakulu onse a ku Yuda ndi Yerusalemu. 2 Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva. 3 Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.
4 Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli. 5 Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. 6 Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba. 7 Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.
8 Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda. 9 Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.
10 Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki. 11 Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.
12 Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni. 13 Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni. 14 Yosiya anaphwanya miyala ya chipembedzo ndiponso anadula mitengo ya fano la Asera ndipo anakwirira malowo ndi mafupa a anthu.
31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.