Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.
63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
kumene kulibe madzi.
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
3 Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
7 Chifukwa ndinu thandizo langa,
ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga umakangamira Inu;
dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;
adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga
ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.
Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Yuda
2 Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?”
Yehova anayankha kuti, “Pita.”
Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?”
Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.”
2 Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli. 3 Davide anatenganso anthu amene anali nawo aliyense ndi banja lake, ndipo anakakhala ku midzi ya ku Hebroni. 4 Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda.
Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli, 5 iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda. 6 Tsopano Yehova akuonetseni kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake ndipo inenso ndidzakukomerani mtima chifukwa munachita zimenezi. 7 Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”
25 “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. 26 Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. 27 Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. 28 Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”
29 Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. 30 Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
31 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” 32 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.
33 “Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.