Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.
3 Inu Yehova, achulukadi adani anga!
Achulukadi amene andiwukira!
2 Ambiri akunena za ine kuti,
“Mulungu sadzamupulumutsa.”
Sela
3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
Sela
5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
7 Dzukani, Inu Yehova!
Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
gululani mano a anthu oyipa.
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
Madalitso akhale pa anthu anu.
Sela
19 Yehova anali ndi Samueli pamene amakula, ndipo zonse zimene ankayankhula zinkachitikadi. 20 Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. 21 Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.
4 Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse.
Afilisti Alanda Bokosi la Chipangano
Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. 2 Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo.
26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.