Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 18:20-30

20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
    molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
    ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
    sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
    ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
    molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.

25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
    kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
    koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
    koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
    Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
    ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
    mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
    kwa onse amene amathawira kwa Iye.

Rute 3:8-18

Tsono pakati pa usiku Bowazi anadzidzimuka, natembenuka, ndipo anangoona mkazi akugona ku mapazi ake.

Iye anafunsa kuti, “Ndiwe yani?” Ndipo anayankha kuti, “Ndine mdzakazi wanu Rute. Popeza ndinu wachibale amene muyenera kundiwombola, ndiye mundilowe chokolo.”

10 Ndipo Bowazi anati, “Mwana wanga, Yehova akudalitse popeza kukoma mtima kumene wasonyeza panoku kwaposa koyamba kaja. Iwe sunathamangire anyamata olemera kapena osauka. 11 Ndipo tsopano mwana wanga usaope. Ine ndidzakuchitira chilichonse udzapemphe popeza anzanga onse amʼmudzi muno akudziwa kuti ndiwe mkazi wa khalidwe labwino. 12 Ngakhale kuti ndinedi wachibale woyenera kukusamala, koma alipo wachibale weniweni kuposa ine. 13 Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.”

14 Choncho Rute anagona ku mapazi ake mpaka mmawa, koma anadzuka mmamawa kusanayere chifukwa Bowazi anati, “Aliyense asadziwe kuti kopondera barele kunabwera mkazi.”

15 Bowazi anati kwa Rute, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho ndipo uchiyale pansi.” Ndipo atayala, Bowazi anathira makilogalamu makumi awiri a barele ndi kumusenzetsa Rute. Rute anapita nakalowa mu mzinda.

16 Rute atafika kwa apongozi ake anamufunsa kuti, “Zinayenda bwanji mwana wanga?” Kenaka iye anafotokoza zonse zimene Bowazi anamuchitira.

17 Ndipo anati, “Munthuyo anandipatsa makilogalamu makumi awiri awa a barele, nandiwuza kuti usapite kwa apongozi ako wopanda kanthu.”

18 Kenaka Naomi anati, “Mwana wanga, dikira mpaka titaona mmene zinthu zikhalire chifukwa munthuyu salekera pomwepo, mpaka zinthuzi zitakonzeka lero.”

Yohane 13:31-35

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32 Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.

33 “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.

34 “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35 Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.