Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 132:1-12

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
    ndi mavuto onse anapirira.

Iye analumbira kwa Yehova
    ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
“Sindidzalowa mʼnyumba mwanga
    kapena kugona pa bedi langa:
sindidzalola kuti maso anga agone,
    kapena zikope zanga ziwodzere,
mpaka nditamupezera malo Yehova,
    malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”

Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata,
    tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
“Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo;
    tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira,
    Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
Ansembe anu avekedwe chilungamo;
    anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”

10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu,
    musakane wodzozedwa wanu.

11 Yehova analumbira kwa Davide,
    lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha:
“Mmodzi wa ana ako
    ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12 ngati ana ako azisunga pangano langa
    ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa,
pamenepo ana awo adzakhala pa mpando
    wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”

Masalimo 132:13-18

13 Pakuti Yehova wasankha Ziyoni,
    Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14 “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi;
    ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15 Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri;
    anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16 Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso,
    ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.

17 “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
    ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18 Ndidzaveka adani ake manyazi,
    koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”

2 Mafumu 22:1-10

Buku la Malamulo Lipezeka

22 Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.

Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati, “Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”

Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga. Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.” 10 Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.

Machitidwe a Atumwi 7:54-8:1

Kuphedwa kwa Stefano

54 Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano. 55 Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. 56 Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”

57 Koma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye, 58 anamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo.

59 Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60 Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.

Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano.

Kuzunzika kwa Mpingo

Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.