Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
146 Tamandani Yehova.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
2 Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.
3 Musamadalire mafumu,
anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.
5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi
Mulungu wa Yakobo.
6 Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
7 Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
8 Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
Yehova amakonda anthu olungama.
9 Yehova amasamalira alendo
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.
Tamandani Yehova.
10 Atamva zimenezi Rute anawerama nazolikitsa nkhope yake pansi. Kenaka anafunsa kuti, “Mwandikomera mtima chotere mlendo ngati ine chifukwa chiyani?”
11 Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse. 12 Yehova akubwezere pa zimene wachitazi. Yehova Mulungu wa Israeli, amene wabwera pansi pa mapiko ake kuti akuteteze, akupatse mphotho yayikulu.”
13 Rute anati, “Mwandikomera mtima, mbuye wanga. Ndipo mwandisangalatsa ndi kundiyankhula mwa chifundo ngakhale sindili mmodzi mwa adzakazi anu.”
14 Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.
Fanizo la Msamariya Wachifundo
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”
Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.