Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Estere 7:1-6

Hamani Aphedwa

Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”

Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”

Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”

Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”

Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi.

Estere 7:9-10

Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”

Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10 Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.

Estere 9:20-22

20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.

Masalimo 124

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    anene tsono Israeli,
akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    potiwukira anthuwo,
iwo atatipsera mtima,
    akanatimeza amoyo;
chigumula chikanatimiza,
    mtsinje ukanatikokolola,
madzi a mkokomo
    akanatikokolola.

Atamandike Yehova,
    amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
    yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
    ndipo ife tapulumuka.
Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Yakobo 5:13-20

Pemphero la Chikhulupiriro

13 Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza. 14 Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. 15 Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. 16 Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

17 Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka. 18 Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake. 19 Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, 20 kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.

Marko 9:38-50

Wosatsutsana Nafe Athandizana Nafe

38 Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”

39 Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine, 40 pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu. 41 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”

Zochimwitsa Ena

42 “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. 43 Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. 44 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 45 Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. 46 (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). 47 Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, 48 kumene

“ ‘mphutsi zake sizifa
    ndipo moto wake suzima.’

49 Aliyense adzayesedwa ndi moto.

50 “Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.