Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 144:9-15

Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu;
    ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
10 kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,
    amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

11 Landitseni ndi kundipulumutsa,
    mʼmanja mwa anthu achilendo,
amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza,
    amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo
    adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,
ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala
    zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza
    ndi zokolola za mtundu uliwonse.
Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda
    pa mabusa athu.
14     Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera.
Sipadzakhala mingʼalu pa makoma,
    sipadzakhalanso kupita ku ukapolo,
    mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

15 Odala anthu amene adzalandira madalitso awa;
    odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

Nyimbo ya Solomoni 5:2-6:3

Mkazi

Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso.
    Tamverani, bwenzi langa akugogoda:
“Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa,
    nkhunda yanga, wangwiro wanga.
Mutu wanga wanyowa ndi mame,
    tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”
Ndavula kale zovala zanga,
    kodi ndizivalenso?
Ndasamba kale mapazi anga
    kodi ndiwadetsenso?
Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko;
    mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.
Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo,
    ndipo manja anga anali noninoni ndi mure,
zala zanga zinali mure chuchuchu,
    pa zogwirira za chotsekera.
Ndinamutsekulira wachikondi wanga,
    koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita.
    Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake.
Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze.
    Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.
Alonda anandipeza
    pamene ankayendera mzindawo.
Anandimenya ndipo anandipweteka;
    iwo anandilanda mwinjiro wanga,
    alonda a pa khoma aja!
Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani,
    mukapeza wokondedwa wangayo,
kodi mudzamuwuza chiyani?
    Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.

Abwenzi

Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,
    kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji?
Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani
    kuti uzichita kutipempha motere?

Mkazi

10 Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi
    pakati pa anthu 1,000.
11 Mutu wake ndi golide woyengeka bwino;
    tsitsi lake ndi lopotanapotana,
    ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.
12 Maso ake ali ngati nkhunda
    mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,
    zitayima ngati miyala yamtengowapatali.
13 Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya
    zopatsa fungo lokoma.
Milomo yake ili ngati maluwa okongola
    amene akuchucha mure.
14 Manja ake ali ngati ndodo zagolide
    zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali.
Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu
    woyikamo miyala ya safiro.
15 Miyendo yake ili ngati mizati yamwala,
    yokhazikika pa maziko a golide.
Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni,
    abwino kwambiri ngati mkungudza.
16 Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri;
    munthuyo ndi wokongola kwambiri!
Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa,
    inu akazi a ku Yerusalemu.

Abwenzi

Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,
    kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti?
Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti
    kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?

Mkazi

Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake,
    ku timinda ta zokometsera zakudya,
akukadyetsa ziweto zake ku minda,
    ndiponso akuthyola maluwa okongola.
Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga;
    amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.

1 Petro 2:19-25

19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.

22 “Iye sanachite tchimo
    kapena kunena bodza.”

23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.