Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
2 Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israeli.
Lemekeza Mulungu
5 Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.
2 Usamafulumire kuyankhula,
usafulumire mu mtima mwako
kunena chilichonse pamaso pa Mulungu.
Mulungu ali kumwamba
ndipo iwe uli pa dziko lapansi,
choncho mawu ako akhale ochepa.
3 Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa,
ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.
4 Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako. 5 Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo. 6 Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako? 7 Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.
Chuma Nʼchopandapake
8 Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa. 9 Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.
10 Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo;
aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza.
Izinso ndi zopandapake.
11 Chuma chikachuluka
akudya nawo chumacho amachulukanso.
Nanga mwini wake amapindulapo chiyani
kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?
12 Wantchito amagona tulo tabwino
ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri,
koma munthu wolemera, chuma
sichimulola kuti agone.
13 Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano:
chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe,
14 kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka,
kotero kuti pamene wabereka mwana
alibe kanthu koti amusiyire.
15 Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake,
ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho.
Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta
palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.
16 Izinso ndi zoyipa kwambiri:
munthu adzapita monga momwe anabwerera,
ndipo iye amapindula chiyani,
pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?
17 Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima,
kukhumudwa kwakukulu, masautso ndi nkhawa.
18 Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake. 19 Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. 20 Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.
Mkangano Woti Yesu Ndani
21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”
22 Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”
23 Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. 24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”
25 Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”
Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, 26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
27 Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. 28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” 30 Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.
Ana a Abrahamu
31 Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. 32 Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
33 Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”
34 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. 35 Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. 36 Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu. 37 Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38 Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.