Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 124

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    anene tsono Israeli,
akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    potiwukira anthuwo,
iwo atatipsera mtima,
    akanatimeza amoyo;
chigumula chikanatimiza,
    mtsinje ukanatikokolola,
madzi a mkokomo
    akanatikokolola.

Atamandike Yehova,
    amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
    yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
    ndipo ife tapulumuka.
Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Estere 1:1-21

Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa

Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.

Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake.

Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero.

10 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11 kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12 Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima.

13 Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14 Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo.

15 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?”

16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18 Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.”

19 “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20 Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.”

21 Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani.

Machitidwe a Atumwi 4:13-31

13 Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu. 14 Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena. 15 Chifukwa chake anawalamula kuti atuluke mʼbwalo la milandu ndipo akulu abwalowo anayamba kukambirana. 16 Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana. 17 Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”

18 Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu. 19 Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20 Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”

21 Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika. 22 Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.

Okhulupirira Apemphera

23 Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza. 24 Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo. 25 Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti,

“ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu,
    ndipo akonzekera kuchita zopandapake?
26 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
    ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
    ndi wodzozedwa wakeyo.’

27 Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza. 28 Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike. 29 Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima. 30 Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”

31 Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.