Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Nyimbo ya Solomoni 2:8-13

Tamverani bwenzi langa!
    Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
    akujowajowa pa zitunda.
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
    Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
    akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
    “Dzuka bwenzi langa,
    wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha;
    mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
    nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
    mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
    mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
    tiye tizipita.”

Masalimo 45:1-2

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.

45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
    pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
    lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.

Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
    ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
    popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.

Masalimo 45:6-9

Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
    ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
    choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
    pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
    kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
    nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
    ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

Yakobo 1:17-27

17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18 Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.

Kumva ndi Kuchita

19 Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20 Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21 Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

22 Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23 Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24 Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25 Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.

26 Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27 Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.

Marko 7:1-8

Miyambo ya Makolo ya Ayuda

Afarisi ndi ena mwa aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anasonkhana momuzungulira Yesu ndipo iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba. (Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo. Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).

Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”

Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti:

“Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
    koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Amandilambira Ine kwachabe;
    ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.

Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”

Marko 7:14-15

14 Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. 15 Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.”

Marko 7:21-23

21 Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, 22 dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. 23 Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.