Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 73:1-20

BUKU LACHITATU

Masalimo 73–89

Salimo la Asafu.

73 Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli,
    kwa iwo amene ndi oyera mtima.

Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka;
    ndinatsala pangʼono kugwa.
Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira,
    pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.

Iwo alibe zosautsa;
    matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu.
Saona mavuto monga anthu ena;
    sazunzika ngati anthu ena onse.
Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo;
    amadziveka chiwawa.
Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa;
    zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.
Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa;
    mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.”
Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba
    ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi.
10 Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo
    ndi kumwa madzi mochuluka.
11 Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji?
    Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?”

12 Umu ndi mmene oyipa alili;
    nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira.

13 Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera;
    pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.
14 Tsiku lonse ndapeza mavuto;
    ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse.

15 Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,”
    ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
16 Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi,
    zinandisautsa kwambiri
17 kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu;
    pamenepo ndinamvetsa mathero awo.

18 Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera;
    Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke.
19 Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa,
    amasesedwa kwathunthu ndi mantha!
20 Monga loto pamene wina adzuka,
    kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye,
    mudzawanyoza ngati maloto chabe.

Miyambo 11

11 Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa,
    koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,
    koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera,
    koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu,
    koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo,
    koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.

Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa,
    koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.

Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso.
    Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.

Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,
    koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.

Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake,
    koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.

10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera,
    ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.

11 Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima,
    koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.

12 Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru,
    koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.

13 Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi;
    koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.

14 Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa;
    koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.

15 Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto,
    koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.

16 Mkazi wodekha amalandira ulemu,
    koma amuna ankhanza amangopata chuma.

17 Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino
    koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.

18 Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu,
    koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.

19 Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo,
    koma wothamangira zoyipa adzafa.

20 Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota
    koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.

21 Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa,
    koma anthu olungama adzapulumuka.

22 Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba,
    ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.

23 Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha,
    koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.

24 Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe;
    wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.

25 Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera;
    iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.

26 Anthu amatemberera womana anzake chakudya,
    koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.

27 Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo,
    koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.

28 Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota,
    koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.

29 Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,
    ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.

30 Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo,
    ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.

31 Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi,
    kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!

Ahebri 12:3-13

Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima. Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.

Mulungu Amalanga Ana ake

Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:

“Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye
    ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda
    ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”

Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. 13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.