Beginning
1 Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.
Dandawulo la Habakuku
2 Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,
koma wosayankha?
Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!”
koma wosatipulumutsa?
3 Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?
Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?
Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;
pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
4 Kotero malamulo anu atha mphamvu,
ndipo chilungamo sichikugwira ntchito.
Anthu oyipa aposa olungama,
kotero apotoza chilungamo.
Yankho la Yehova
5 “Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani,
ndipo muthedwe nazo nzeru.
Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu
zimene inu simudzazikhulupirira,
ngakhale wina atakufotokozerani.
6 Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni,
anthu ankhanza ndiponso amphamvu,
amene amapita pa dziko lonse lapansi
kukalanda malo amene si awo.
7 Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa;
amadzipangira okha malamulo
ndi kudzipezera okha ulemu.
8 Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku
ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo.
Okwerapo awo akuthamanga molunjika;
a pa akavalo awo ndi ochokera kutali,
akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
9 onse akubwera atakonzekera zachiwawa.
Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu
ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
10 Akunyoza mafumu
ndiponso kuchitira chipongwe olamulira.
Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa;
akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.
11 Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe,
anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”
Dandawulo Lachiwiri la Habakuku
12 Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire?
Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa.
Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo;
Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
13 Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa;
Inu simulekerera cholakwa.
Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa?
Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa
akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
14 Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,
ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.
15 Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza,
amawakola mu ukonde wake,
amawasonkhanitsa mu khoka lake;
kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.
16 Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake
ndiponso kufukizira lubani khoka lake,
popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba
ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
17 Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo,
kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?
2 Ndidzakhala pa malo anga aulonda,
ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo;
ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze,
ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.
Yankho la Yehova
2 Tsono Yehova anandiyankha, nati:
“Lemba masomphenyawa
ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale
kuti wowerenga awawerenge mosavuta.
3 Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;
masomphenyawa akunena zamʼtsogolo
ndipo sizidzalephera kuchitika.
Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;
zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.
4 “Taona, mdani wadzitukumula;
zokhumba zake sizowongoka,
koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
5 Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo;
ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika.
Pakuti ngodzikonda ngati manda,
ngosakhutitsidwa ngati imfa,
wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu
ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse.
6 “Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti,
“Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake
ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda!
Kodi izi zidzachitika mpaka liti?
7 Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi?
Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha?
Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.
8 Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu,
mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo.
Pakuti wakhetsa magazi a anthu;
wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
9 “Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo,
kukweza malo ake okhalapo,
kuthawa mavuto!
10 Wakonzekera kuwononga mitundu yambiri ya anthu,
kuchititsa manyazi nyumba yako yomwe ndi kuwononga moyo wako.
11 Mwala pa khoma udzafuwula,
ndipo mitanda ya matabwa idzavomereza zimenezi.
12 “Tsoka kwa amene amanga mzinda pokhetsa magazi
ndi kukhazikitsa mzinda pochita zoyipa!
13 Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize
kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto,
ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu?
14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova,
monga momwe madzi amadzazira nyanja.
15 “Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zakumwa zoledzeretsa,
kutsanula mʼbotolo mpaka ataledzera,
kuti aone umaliseche wawo.
16 Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero.
Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere!
Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe,
ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
17 Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni,
ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga.
Pakuti wakhetsa magazi a anthu;
wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
18 “Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu,
kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza?
Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake;
amapanga mafano amene samatha kuyankhula.
19 Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’
Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’
Kodi zimenezi zingathe kulangiza?
Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva;
mʼkati mwake mulibe mpweya.
20 Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika;
dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.”
Pemphero la Habakuku
3 Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.
2 Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;
Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.
Muzichitenso masiku athu ano,
masiku athu ano zidziwike;
mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.
3 Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,
Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.
Sela
Ulemerero wake unaphimba mlengalenga
ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
4 Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;
kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,
mʼmene anabisamo mphamvu zake.
5 Patsogolo pake pankagwa mliri;
nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.
6 Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;
anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.
Mapiri okhazikika anagumuka
ndipo zitunda zakalekale zinatitimira.
Njira zake ndi zachikhalire.
7 Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,
mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.
8 Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?
Kodi munakalipira timitsinje?
Kodi munapsera mtima nyanja
pamene munakwera pa akavalo anu
ndiponso magaleta anu achipulumutso?
9 Munasolola uta wanu mʼchimake,
munayitanitsa mivi yambiri.
Sela
Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;
10 mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.
Madzi amphamvu anasefukira;
nyanja yozama inakokoma
ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.
11 Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,
pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,
pa kunyezimira kwa mkondo wanu.
12 Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,
ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.
13 Munapita kukalanditsa anthu anu,
kukapulumutsa wodzozedwa wanu.
Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,
munawononga anthu ake onse.
Sela
14 Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake
pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa,
ankasangalala ngati kuti akudzawononga
osauka amene akubisala.
15 Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,
kuvundula madzi amphamvu.
16 Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri,
milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo;
mafupa anga anaguluka,
ndipo mawondo anga anawombana.
Komabe ndikuyembekezera mofatsa,
tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.
17 Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,
ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.
Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,
ndipo mʼminda musatuluke kanthu.
Ngakhale nkhosa
ndi ngʼombe zithe mʼkhola,
18 komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,
ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.
19 Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;
amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,
amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.
1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.
Yehova Adzaweruza Dziko Lapansi
2 “Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse
pa dziko lapansi,”
akutero Yehova.
3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe;
ndidzawononga mbalame zamlengalenga
ndi nsomba za mʼnyanja.
Ndidzawononga anthu oyipa,
ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,”
akutero Yehova.
Chenjezo kwa Yuda
4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda
ndi onse okhala mu Yerusalemu.
Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala,
mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:
5 amene amagwada pa madenga a nyumba zawo
kupembedza zolengedwa zamumlengalenga,
amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova,
komanso mʼdzina la Moleki,
6 amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova,
osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova.
7 Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova,
chifukwa tsiku la Yehova layandikira.
Yehova wakonzekera kupereka nsembe;
wapatula iwo amene wawayitana.
8 Pa tsiku la nsembe ya Yehova
ndidzalanga akalonga
ndi ana aamuna a mfumu
ndi onse amene amavala
zovala zachilendo.
9 Pa tsiku limenelo ndidzalanga
onse amene safuna kuponda pa chiwundo,
amene amadzaza nyumba ya ambuye awo
ndi chiwawa ndi chinyengo.
10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova,
“Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba,
kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano,
ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.
11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika;
a malonda anu onse adzapululidwa,
ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.
12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale
ndi kulanga onse amene sakulabadira,
amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa,
amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse,
chabwino kaya choyipa.’
13 Chuma chawo chidzafunkhidwa,
nyumba zawo zidzagwetsedwa.
Adzamanga nyumba,
koma osakhalamo;
adzadzala minda ya mpesa
koma sadzamwako vinyo wake.”
Tsiku Lalikulu la Yehova
14 Tsiku lalikulu la Yehova layandikira,
layandikira ndipo lifika msanga.
Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa,
ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.
15 Tsiku limenelo lidzakhala la ukali,
tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni,
tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko,
tsiku la mdima ndi lachisoni,
tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
16 Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo,
tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa
ndi nsanja za pa ngodya.
17 Ndidzabweretsa msautso pa anthu
ndipo adzayenda ngati anthu osaona,
chifukwa achimwira Yehova,
magazi awo adzamwazika ngati fumbi
ndi mnofu wawo ngati ndowe.
18 Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo
sadzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Dziko lonse lapansi lidzanyeka
mʼmoto wa nsanje yake
chifukwa adzakantha modzidzimutsa
onse okhala pa dziko lapansi.
2 Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi,
inu mtundu wochititsa manyazi,
2 isanafike nthawi yachiweruzo,
nthawi yanu isanawuluke ngati mungu,
usanakufikeni mkwiyo woopsa wa Yehova,
tsiku la ukali wa Yehova lisanafike pa inu.
3 Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko,
inu amene mumachita zimene amakulamulani.
Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa;
mwina mudzatetezedwa
pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Za Afilisti
4 Gaza adzasiyidwa
ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja.
Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu
ndipo Ekroni adzazulidwa.
5 Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja,
inu mtundu wa Akereti;
mawu a Yehova akutsutsa
iwe Kanaani, dziko la Afilisti.
“Ndidzakuwononga
ndipo palibe amene adzatsale.”
6 Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti,
lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.
7 Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda;
adzapezako msipu.
Nthawi ya madzulo adzagona
mʼnyumba za Asikeloni.
Yehova Mulungu wawo adzawasamalira;
adzabwezeretsa mtendere wawo.
Za Mowabu ndi Amoni
8 “Ndamva kunyoza kwa Mowabu
ndi chipongwe cha Amoni,
amene ananyoza anthu anga
ndi kuopseza kuti alanda dziko lawo.
9 Choncho, pali Ine Wamoyo,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,
“Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu,
Amoni adzasanduka ngati Gomora;
malo a zomeramera ndi maenje a mchere,
dziko la bwinja mpaka muyaya.
Anthu anga otsala adzawafunkha;
opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
10 Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo,
chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.
11 Yehova adzawachititsa mantha kwambiri
pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo.
Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira,
uliwonse ku dziko la kwawo.
Za Kusi
12 “Inunso anthu a ku Kusi,
mudzaphedwa ndi lupanga.”
Za Asiriya
13 Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto
ndi kuwononga Asiriya,
kusiya Ninive atawonongekeratu
ndi owuma ngati chipululu.
14 Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko,
pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse.
Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu
adzakhala pa nsanamira zake.
Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera,
mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha,
nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
15 Umenewu ndiye mzinda wosasamala
umene kale unali wotetezedwa.
Unkanena kuti mu mtima mwake,
“Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.”
Taonani lero wasanduka bwinja,
kokhala nyama zakutchire!
Onse owudutsa akuwunyoza
ndi kupukusa mitu yawo.
Tsogolo la Yerusalemu
3 Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza,
owukira ndi odetsedwa!
2 Sumvera aliyense,
sulandira chidzudzulo.
Sumadalira Yehova,
suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.
3 Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma,
olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo,
zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.
4 Aneneri ake ndi odzikuza;
anthu achinyengo.
Ansembe ake amadetsa malo opatulika
ndipo amaphwanya lamulo.
5 Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama;
Iye salakwa.
Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama,
ndipo tsiku lililonse salephera,
komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
6 “Ndachotseratu mitundu ya anthu;
ndagwetsa malinga awo.
Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo,
popanda aliyense wodutsa.
Mizinda yawo yawonongedwa;
palibe aliyense adzatsalemo.
7 Ndinati,
‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa
ndi kumvera kudzudzula kwanga!’
Ndipo sindidzawononga nyumba zawo,
kapena kuwalanganso.
Koma iwo anali okonzeka
kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
8 Choncho mundidikire,” akutero Yehova,
“chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni.
Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu,
kusonkhanitsa maufumu
ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo;
mkwiyo wanga wonse woopsa.
Dziko lonse lidzatenthedwa
ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.
9 “Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse
kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova
ndi kumutumikira Iye pamodzi.
10 Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi
anthu anga ondipembedza, omwazikana,
adzandibweretsera zopereka.
11 Tsiku limenelo simudzachita manyazi
chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira,
popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu
amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo.
Simudzakhalanso odzikuza
mʼphiri langa lopatulika.
12 Koma ndidzasiya pakati panu
anthu ofatsa ndi odzichepetsa,
amene amadalira dzina la Yehova.
13 Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika;
sadzayankhulanso zonama,
ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo.
Adzadya ndi kugona
ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”
14 Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni;
fuwula mokweza, iwe Israeli!
Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse,
iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
15 Yehova wachotsa chilango chako,
wabweza mdani wako.
Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako;
sudzaopanso chilichonse.
16 Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,
“Usaope, iwe Ziyoni;
usafowoke.
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako,
ali ndi mphamvu yopulumutsa.
Adzakondwera kwambiri mwa iwe,
adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,
adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
18 “Ndidzakuchotserani zowawa
za pa zikondwerero zoyikika;
nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.
19 Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi
onse amene anakuponderezani;
ndidzapulumutsa olumala
ndi kusonkhanitsa amene anamwazika.
Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu
mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
20 Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani;
pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu.
Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu
pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi
pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu
inu mukuona,”
akutero Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.