Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 46-48

46 “Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Mfumu izilowa podzera mʼkhonde la mʼkati la chipata pochokera kunja, nʼkudzayima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pa chiwundo cha pa chipatacho kenaka nʼkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo. Anthu a mʼdziko azipembedza pamaso pa Yehova pa khomo la chipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa tsiku la mwezi watsopano. Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Yehova ikhale motere: pa tsiku la Sabata izipereka ana ankhosa aamuna asanu ndi mmodzi wopanda chilema, ndiponso nkhosa yayima yopanda chilema. Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu. Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema. Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta. Pamene mfumu ikulowa, izidzera mʼkhonde lamʼkati la chipata chakummawa, izitulukiranso pomwepo.

“Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho. 10 Mfumu izidzakhala pakati pawo. Anthu akamadzalowa mfumu idzalowa nawo. Anthu akamadzatuluka mfumu idzatuluka nawo.

11 “Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse. 12 Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.

13 “Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi. 14 Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo. 15 Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku.

16 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo. 17 Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake. 18 Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’ ”

19 Kenaka munthu uja anandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandilowetsa ku zipinda za ansembe zoyangʼana kumpoto. Ndipo ndinaona kumeneko malo chakumadzulo kwa zipindazo. 20 Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”

21 Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina. 22 Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu. 23 Kuzungulira mabwalo anayi angʼonoangʼono aja panali mpanda wamiyala, ndi malo asonkhapo moto omangidwa mʼmunsi mwa mpandawo mozungulira. 24 Munthuyo anandiwuza kuti, “Izi ndi zipinda zophikiramo. Mʼmenemu anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzaphikiramo nyama za nsembe za anthu.”

Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu

47 Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.

Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”

Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10 Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11 Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12 Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”

Malire a Dziko

13 Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. 14 Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.

15 “Malire a dzikolo adzakhala motere:

Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, 16 Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. 17 Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.

18 Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.

19 Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.

20 Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.”

21 “Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. 22 Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. 23 Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

Magawidwe ka Dziko

48 “Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.

“Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

“Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.

“Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 10 Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. 11 Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera. 12 Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.

13 “Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 14 Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.

15 “Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati. 16 Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250. 17 Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125. 18 Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda. 19 Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli. 20 Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.

21 “Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu. 22 Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.

23 “Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.

24 “Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

25 “Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

26 “Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

27 “Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.

28 “Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.

29 “Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.

Zipata za Mzinda

30 “Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250, 31 kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.

32 “Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.

33 “Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.

34 “Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.

35 “Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000.

“Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala:

Yehova Ali Pano.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.