Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 28-30

Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo

28 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza
    umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;
ndimakhala pa mpando wa mulungu
    pakati pa nyanja.’
Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,
    ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.
    Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako
    unadzipezera chuma
ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva
    mʼnyumba zosungira chuma chako.
Ndi nzeru zako zochitira malonda
    unachulukitsa chuma chako
ndipo wayamba kunyada
    chifukwa cha chuma chakocho.

“ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Popeza umadziganizira
    kuti ndiwe mulungu,
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,
    kuti adzalimbane nawe.
Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,
    ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
Iwo adzakuponyera ku dzenje
    ndipo udzafa imfa yoopsa
    mʼnyanja yozama.
Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’
    pamaso pa iwo amene akukupha?
Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,
    mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
10 Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe
    mʼmanja mwa anthu achilendo.

Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”

11 Yehova anandiyankhula kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,
    wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
13 Iwe unkakhala ngati mu Edeni,
    munda wa Mulungu.
Miyala yokongola ya mitundu yonse:
    rubi, topazi ndi dayimondi,
    kirisoliti, onikisi, yasipa,
    safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.
Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.
    Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
14 Ndinayika kerubi kuti azikulondera.
    Unkakhala pa phiri langa lopatulika,
ndipo unkayendayenda
    pakati pa miyala ya moto.
15 Makhalidwe ako anali abwino
    kuyambira pamene unalengedwa
    mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
16 Unatanganidwa ndi zamalonda.
    Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu
    ndi kumachimwa.
Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.
    Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa
    kukuchotsa ku miyala yamoto.
17 Unkadzikuza mu mtima mwako
    chifukwa cha kukongola kwako,
ndipo unayipitsa nzeru zako
    chifukwa chofuna kutchuka.
Kotero Ine ndinakugwetsa pansi
    kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18 Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.
    Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.
Choncho ndinabutsa moto pakati pako,
    ndipo unakupsereza,
ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi
    pamaso pa anthu onse amene amakuona.
19 Anthu onse amitundu amene ankakudziwa
    akuchita mantha chifukwa cha iwe.
Watheratu mochititsa mantha
    ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”

Za Chilango cha Sidoni

20 Yehova anandiyankhula nati: 21 “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, 22 ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,
    ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.
Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova
    ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti
    ndine woyera pakati pako.
23 Ndidzatumiza mliri pa iwe
    ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.
Anthu ophedwa ndi lupanga
    adzagwa mbali zonse.
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24 “ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25 “ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”

Za Chilango cha Igupto

29 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
    iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
    ndinadzipangira ndekha.’
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
    ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
    pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
Ndidzakutaya ku chipululu,
    iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
    popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
    cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.

Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.

“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.

13 “ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”

Mphotho ya Nebukadinezara

17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.

21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Za Kulangidwa kwa Igupto

30 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.

“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,
    ‘Kalanga, tsiku lafika!’
Pakuti tsiku layandikira,
    tsiku la Yehova lili pafupi,
tsiku la mitambo yakuda,
    tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
    ndipo mavuto adzafika pa Kusi.
Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,
    chuma chake chidzatengedwa
    ndipo maziko ake adzagumuka.

Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa
    ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.
Adzaphedwa ndi lupanga
    kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”
            ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
    kupambana mabwinja ena onse opasuka,
ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka
    kupambana mizinda ina yonse.
Nditatha kutentha Igupto
    ndi kupha onse omuthandiza,
    pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.

10 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni
    kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
    adzabwera kudzawononga dzikolo.
Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto
    ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
    ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.
Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo
    pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.

Ine Yehova ndayankhula.

13 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzawononga mafano
    ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.
Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,
    ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
    ndi kutentha mzinda wa Zowani.
    Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
    linga lolimba la Igupto,
    ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
    Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
    ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
    adzaphedwa ndi lupanga
    ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
    pamene ndidzathyola goli la Igupto;
    motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
    ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
    ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Farao Watha Mphamvu

20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.