Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Danieli 1-3

Maphunziro a Danieli ku Babuloni

Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo. Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.

Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka, achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni. Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu.

Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. Mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina atsopano: Danieli anamutcha Belitesezara; Hananiya anamutcha Sadirake; Misaeli anamutcha Mesaki; ndi Azariya anamutcha Abedenego.

Koma Danieli anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya ndi vinyo wa mfumu, ndipo anapempha chilolezo kwa mkulu wa nduna za mfumu kuti asadzidetse mwa njira imeneyi. Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli, 10 koma ndunayo inamuwuza Danieli kuti, “Ine ndikuchita mantha ndi mbuye wanga mfumu, amene wapereka chakudya ndi chakumwa chanu. Kodi akuoneni inu owonda kuposa anzanu a misinkhu yanu pa chifukwa chanji? Mfumu ikhoza kundidula mutu chifukwa cha iwe.”

11 Ndipo Danieli anati kwa kapitawo amene anali mkulu wa nduna za mfumu amene anamuyika kuti ayangʼanire Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya, 12 “Chonde mutiyese ife akapolo anu pa masiku khumi: mutipatse masamba okha kuti tidye ndi madzi akumwa. 13 Ndipo mudzafananize maonekedwe athu ndi a anyamata amene akudya chakudya cha mfumu, ndi kuti mudzachite ndi anyamata anu monga momwe mudzawaonere.” 14 Choncho anawavomera ndipo anawayesa pa masiku khumi.

15 Pakutha pa masiku khumi iwo anaoneka athanzi ndi odya bwino kuposa aliyense wa anyamata amene ankadya chakudya cha mfumu aja. 16 Choncho kapitawo anawachotsera chakudya ndi vinyo za ku nyumba yaufumu zija nawapatsa ndiwo zamasamba basi.

17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.

18 Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara. 19 Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu. 20 Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.

21 Ndipo Danieli anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Koresi.

Maloto a Nebukadinezara

Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona. Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”

Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”

Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja. Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”

Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.”

Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita. Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”

10 Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. 11 Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”

12 Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe. 13 Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe.

14 Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni. 15 Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli. 16 Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake.

17 Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 18 Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni. 19 Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba, 20 ndipo anati:

“Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi;
    nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake.
21 Amasintha nthawi ndi nyengo;
    amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso.
Amapatsa nzeru kwa anzeru
    ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.
22 Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika;
    amadziwa zimene zili mu mdima,
    ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.
23 Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga:
    mwandipatsa nzeru ndi mphamvu,
mwandiwululira zomwe tinakupemphani,
    mwatiwululira maloto a mfumu.”

Danieli Atanthauzira Maloto

24 Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.”

25 Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.”

26 Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?”

27 Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, 28 koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:

29 “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. 30 Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.

31 “Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe. 32 Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa. 33 Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo. 34 Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya. 35 Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.

36 “Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. 37 Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero; 38 Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.

39 “Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. 40 Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. 41 Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. 42 Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka. 43 Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo.

44 “Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya. 45 Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa.

“Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”

46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani. 47 Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”

48 Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru. 49 Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.

Fano la Golide ndi Ngʼanjo ya Moto

Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija. Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati:

“Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.”

Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika.

Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda. Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 10 Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, 11 ndi kuti aliyense osalambira ndi kupembedza adzaponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.”

13 Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, 14 ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? 15 Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”

16 Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. 17 Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. 18 Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.”

19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, 20 ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. 21 Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 22 Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, 23 ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.

24 Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?”

Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.”

25 Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.”

26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!”

Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, 27 ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto.

28 Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo. 29 Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.”

30 Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.