Beginning
Makolo a Yesu Khristu Monga mwa Thupi
1 Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
2 Abrahamu anabereka Isake,
Isake anabereka Yakobo,
Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.
3 Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.
Perezi anabereka Hezironi,
Hezironi anabereka Aramu.
4 Aramu anabereka Aminadabu,
Aminadabu anabereka Naasoni,
Naasoni anabereka Salimoni.
5 Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,
Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute,
Obedi anabereka Yese.
6 Yese anabereka Mfumu Davide.
Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.
7 Solomoni anabereka Rehabiamu,
Rehabiamu anabereka Abiya,
Abiya anabereka Asa,
8 Asa anabereka Yehosafati,
Yehosafati anabereka Yoramu,
Yoramu anabereka Uziya.
9 Uziya anabereka Yotamu,
Yotamu anabereka Ahazi,
Ahazi anabereka Hezekiya.
10 Hezekiya anabereka Manase,
Manase anabereka Amoni,
Amoni anabereka Yosiya.
11 Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.
12 Ali ku ukapolo ku Babuloni,
Yekoniya anabereka Salatieli,
Salatieli anabereka Zerubabeli.
13 Zerubabeli anabereka Abiudi,
Abiudi anabereka Eliakimu,
Eliakimu anabereka Azoro.
14 Azoro anabereka Zadoki,
Zadoki anabereka Akimu,
Akimu anabereka Eliudi.
15 Eliudi anabereka Eliezara,
Eliezara anabereka Matani,
Matani anabereka Yakobo.
16 Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.
17 Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.
Kubadwa kwa Yesu Khristu
18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.
20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”
22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23 “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”
24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.
Anzeru a Kummawa
2 Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu 2 nafunsa kuti, “Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza.”
3 Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. 4 Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, “Kodi Khristu adzabadwira kuti?” 5 Ndipo anamuyankha kuti, “Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,
6 “ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya,
sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya;
pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe,
amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”
7 Pomwepo Herode anawayitanira mseri Anzeruwo nawafunsitsa nthawi yeniyeni yomwe nyenyeziyo inaoneka. 8 Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, “Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze.”
9 Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo. 10 Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11 Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure. 12 Ndipo atachenjezedwa mʼmaloto kuti asapitenso kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwawo podzera njira ina.
Athawira ku Igupto
13 Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.” 14 Atadzuka, Yosefe anatenga mwanayo ndi amayi ake usiku omwewo napita ku Igupto, 15 nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”
Kuphedwa kwa Ana mʼBetelehemu
16 Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza. 17 Pamenepo, zimene ananena mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa:
18 “Kulira kukumveka ku Rama,
kubuma ndi kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake;
sakutonthozeka,
chifukwa ana akewo palibe.”
Abwerera ku Nazareti
19 Atamwalira Herode, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto ku Igupto 20 nanena kuti, “Nyamuka, tenga mwanayo ndi amayi ake ndipo mupite ku dziko la Israeli, popeza amene anafuna moyo wa mwanayo anamwalira.”
21 Tsono Yosefe atadzuka anatenga mwanayo ndi amayi ake kupita ku dziko la Israeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao akulamulira mu Yudeya mʼmalo mwa abambo ake, Herode, anaopa kupitako. Atachenjezedwa mʼmaloto, anapita ku Galileya, 23 ndipo anakakhazikika mu mzinda wa Nazareti. Pamenepo zinakwaniritsidwa zonenedwa ndi aneneri kuti, “Adzatchedwa Mnazareti.”
Yohane Mʼbatizi
3 Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya 2 kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” 3 Uyu ndi amene mneneri Yesaya ananena za iye kuti,
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ ”
4 Zovala za Yohane zinali zopangidwa ndi ubweya wa ngamira, ndipo amamangira lamba wachikopa mʼchiwuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. 5 Anthu ankapita kwa iye kuchokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndi ku madera onse a Yorodani. 6 Ndipo akavomereza machimo awo ankabatizidwa mu mtsinje wa Yorodani.
7 Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera? 8 Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima. 9 Ndipo musaganize ndi kunena mwa inu nokha kuti, ‘Tili nawo abambo athu Abrahamu.’ Ndinena kwa inu kuti Mulungu akhoza kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abrahamu. 10 Tikukamba pano nkhwangwa yayikidwa kale pa mizu ya mitengo, ndipo mtengo umene subala chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa pa moto.
11 “Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto. 12 Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”
Kubatizidwa kwa Yesu
13 Pamenepo Yesu anabwera kuchokera ku Galileya kudzabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 14 Koma Yohane anayesetsa kumukanira nati, “Ndiyenera kubatizidwa ndi Inu, bwanji Inu mubwera kwa ine?”
15 Yesu anayankha kuti, “Zibatero tsopano, ndi koyenera kwa ife kuchita zimenezi kukwaniritsa chilungamo chonse.” Ndipo Yohane anavomera.
16 Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye. 17 Ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa amene ndikondwera naye.”
Yesu Ayesedwa Mʼchipululu
4 Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. 2 Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala. 3 Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”
5 Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. 6 Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:
“ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,
ndipo adzakunyamula ndi manja awo
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”
7 Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
8 Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. 9 Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”
10 Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
Yesu Ayamba Kulalikira
12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya. 13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali; 14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,
Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 anthu okhala mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa
kuwunika kwawafikira.”
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Odwala
23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu. 24 Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa. 25 Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.