Beginning
Za Kuweruza Ena
7 “Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. 2 Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.
3 “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? 4 Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako? 5 Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako.
6 “Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.
Pemphani, Funafunani, Gogodani
7 “Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. 8 Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
9 “Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? 10 Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? 11 Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha? 12 Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.
Zipata Ziwiri ndi Njira Ziwiri
13 “Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. 14 Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.
Aneneri Owona ndi Onyenga
15 “Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? 17 Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa. 18 Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino. 19 Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. 20 Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.
Ophunzira Owona ndi Onyenga
21 “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. 22 Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ 23 Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’
Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa
24 “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26 Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. 27 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”
28 Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29 chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.
Yesu Achiritsa Wakhate
8 Iye atatsika ku phiri kuja, anthu ambirimbiri anamutsata. 2 Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, “Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
3 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake. 4 Ndipo Yesu anati kwa iye, “Taona, usawuze wina aliyense. Koma upite kwa mkulu wa ansembe ukadzionetse wekha ndi kupereka mphatso imene Mose analamulira, kuti ukhale umboni kwa iwo.”
Chikhulupiriro cha Kenturiyo
5 Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, 6 nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”
7 Ndipo Yesu anati kwa iye, “Ine ndibwera kudzamuchiritsa.”
8 Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. 9 Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”
10 Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere. 11 Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. 12 Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
13 Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, “Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira.” Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
14 Ndipo Yesu atalowa mʼnyumba ya Petro, anaona mpongozi wake wa Petro ali gone akudwala malungo. 15 Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.
16 Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. 17 Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,
“Iye anatenga zofowoka zathu,
nanyamula nthenda zathu.”
Za Kutsatira Yesu
18 Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. 19 Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”
20 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”
21 Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”
22 Koma Yesu anamuwuza kuti, “Nditsate Ine ndipo uwaleke akufa ayikane akufa okhaokha.”
Yesu Aletsa Namondwe
23 Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24 Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25 Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”
26 Iye anawayankha kuti, “Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?” Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.
27 Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”
Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara
28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29 Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”
30 Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31 Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”
32 Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. 33 Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.