Beginning
Fanizo la Wofesa
8 Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye, 2 komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri; 3 Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo.
4 Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili, 5 “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. 6 Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. 7 Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. 8 Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.”
Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”
9 Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. 10 Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti,
“ngakhale akuona, asapenye;
ngakhale akumva, asazindikire.”
11 “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12 Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. 13 Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. 14 Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. 15 Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.
Nyale ndi Choyikapo Chake
16 “Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala. 17 Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikadzawululika, ndipo palibe kanthu kophimbika kamene sikadzadziwika kapena kuonetsedwa poyera. 18 Choncho ganizirani mozama. Iye amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, iye amene alibe, ngakhale chimene akuganiza kuti ali nacho adzalandidwa.”
Amayi ndi Abale a Yesu
19 Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu. 20 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.”
21 Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”
Yesu Aletsa Namondwe
22 Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. 23 Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.
24 Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!”
Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. 25 Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Chikhulupiriro chanu chili kuti?”
Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye.”
Achiritsidwa Munthu Wogwidwa ndi Ziwanda
26 Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya. 27 Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda. 28 Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!” 29 Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.
30 Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?”
Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. 31 Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.
32 Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola. 33 Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.
34 Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. 35 Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha. 36 Amene anaona izi anawuza anthu mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anachiritsidwira. 37 Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka.
38 Munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja, anapempha Yesu kuti apite nawo, koma Yesu anamubweza nati, 39 “Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.
Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu
40 Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. 41 Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, 42 chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa.
Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza. 43 Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. 44 Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
45 Yesu anafunsa kuti, “Wandikhudza ndani?”
Onse atakana, Petro anati, “Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani.”
46 Koma Yesu anati, “Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine.”
47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48 Kenaka anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”
49 Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.”
50 Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, “Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa.”
51 Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. 52 Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”
53 Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. 54 Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, “Mwana wanga, dzuka!” 55 Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. 56 Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.
Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri
9 Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. 2 Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. 3 Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. 4 Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo. 5 Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.” 6 Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.
7 Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa, 8 ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. 9 Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
10 Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida. 11 Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
13 Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.”
Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.” 14 (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000).
Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.” 15 Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. 16 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. 17 Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
Petro Avomereza Khristu
18 Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
19 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
20 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
Yesu Aneneratu za Imfa yake
21 Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. 22 Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
23 Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. 24 Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. 25 Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? 26 Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera. 27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
28 Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. 29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. 30 Anthu awiri, Mose ndi Eliya, 31 anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu. 32 Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye. 33 Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
34 Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta. 35 Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.” 36 Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
Kuchiritsidwa kwa Mwana Wogwidwa ndi Chiwanda
37 Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye. 38 Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. 39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. 40 Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.”
41 Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. 43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.
Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake
Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake, 44 “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.” 45 Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.
Wamkulu Ndani?
46 Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo. 47 Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake. 48 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
49 Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
50 Yesu anati, “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”
A Samariya Akana Yesu
51 Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu, 52 ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira, 53 koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. 54 Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?” 55 Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula, 56 ndipo iwo anapita ku mudzi wina.
Kutsatira Yesu
57 Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
58 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”
59 Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.”
Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
60 Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”
61 Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.”
62 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.