Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mateyu 18-19

Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba

18 Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, “Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?”

Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba. Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.

Za Kuchimwitsa Ena

“Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja. Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zimene ziyenera kubwera, koma tsoka kwa munthu amene abweretsa zotere! Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.”

Fanizo la Nkhosa Yotayika

10 “Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.” 11 (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika).

12 “Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo? 13 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. 14 Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

15 “Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. 16 Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’ 17 Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.

18 “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.

19 “Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. 20 Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”

Fanizo la Wantchito Wopanda Chifundo

21 Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?”

22 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri.

23 “Nʼchifukwa chake, ufumu wakumwamba ukufanana ndi mfumu imene inafuna kuti antchito ake abweze ngongole. 24 Atangoyamba kulandira, anamubweretsa munthu kwa iye amene anakongola ndalama 10,000. 25 Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.

26 “Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’ 27 Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite.

28 “Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’

29 “Wantchito mnzakeyo anagwada namupempha iye kuti, ‘Lezere mtima ine, ndipo ndidzakubwezera.’

30 “Koma iye anakana. Mʼmalo mwake, anachoka nakamumangitsa kufikira atabweza ngongoleyo. 31 Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika.

32 “Pamenepo bwanayo anayitana wantchitoyo nati, ‘Iwe wantchito woyipa mtima, ndinakukhululukira ngongole yako yonse chifukwa unandipempha. 33 Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’ 34 Ndi mkwiyo, bwana wakeyo anamupereka kwa oyangʼanira ndende kuti amuzuze mpaka atabweza zonse zimene anakongola.

35 “Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”

Za Kuthetsa Ukwati

19 Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo.

Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, “Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?”

Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”

Ndipo iwo anamufunsa nati, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?”

Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”

10 Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”

11 Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. 12 Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”

Yesu Adalitsa Ana

13 Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.

14 Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.” 15 Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.

Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu

16 Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”

17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”

18 Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”

Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19 lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”

20 Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?”

21 Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”

22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

23 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”

25 Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?”

26 Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

27 Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”

28 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. 30 Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.