Beginning
Munthu Wakufa Ziwalo wa ku Kaperenawo
9 Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo. 2 Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
3 Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”
4 Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, “Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? 5 Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ 6 Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ” 7 Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo. 8 Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu.
Kuyitanidwa kwa Mateyu
9 Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, “Nditsate Ine.” Ndipo iye ananyamuka namutsata.
10 Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11 Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, “Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”
12 Yesu atamva, anati, “Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala. 13 Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa.”
Za Kusala Kudya
14 Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”
15 Yesu anayankha kuti, “Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.”
16 Ndipo palibe munthu amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale chifukwa chigambacho chidzachoka ndipo chibowocho chidzakula kuposa kale. 17 Kapena sathira vinyo watsopano mʼmatumba akale; akatero, matumba akalewo adzaphulika ndipo vinyoyo adzatayika, matumbawo adzawonongeka; satero ayi. Amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso ndipo zonse zimasungika.
Za Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu
18 Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.” 19 Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi.
20 Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake. 21 Iyeyo anati mwa iye yekha, “Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa.”
22 Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati, “Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa.
23 Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso, 24 anati, “Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye. 25 Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka. 26 Mbiriyi inamveka mʼdera lonse.
Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula
27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”
28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?”
Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”
29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.
32 Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. 33 Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”
34 Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.”
Antchito ndi Ochepa
35 Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo. 36 Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa. 37 Pamenepo anati kwa ophunzira ake, “Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa. 38 Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”
Yesu Atuma Ophunzira Ake
10 Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.
2 Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane, 3 Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; 4 Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
5 Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. 6 Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. 7 Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ 8 Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.
9 “Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.
16 “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17 Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18 Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19 Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20 pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.
21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.
24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!
26 “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27 Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29 Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31 Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
32 “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.
34 “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35 Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa
“ ‘Munthu ndi abambo ake,
mwana wamkazi ndi amayi ake,
mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,
36 adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’
37 “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38 Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39 Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.
40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.