Beginning
Yesu Atuma Ophunzira 72
10 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. 2 Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola. 3 Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.
5 “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ 6 Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu. 7 Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.
8 “Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani. 9 Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 10 Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti, 11 ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12 Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.
13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 14 Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu. 15 Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.
16 “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”
17 Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.”
18 Iye anayankha kuti, “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi. 19 Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani. 20 Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”
21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.
22 “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”
23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi. 24 Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”
Fanizo la Msamariya Wachifundo
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”
Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
Marita ndi Mariya
38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. 39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. 40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!”
41 Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri, 42 koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”
Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera
11 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
2 Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti:
“ ‘Atate,
dzina lanu lilemekezedwe,
ufumu wanu ubwere.
3 Mutipatse chakudya chathu chalero,
4 mutikhululukire machimo athu,
monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.
Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”
5 Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, 6 chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’
7 “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ 8 Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.
9 “Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.
11 “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”
Yesu ndi Belezebabu
14 Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. 15 Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.” 16 Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba.
17 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka. 18 Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu. 19 Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu. 20 Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.
21 “Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa. 22 Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.
23 “Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.
Za Mzimu Woyipa
24 “Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’ 25 Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza. 26 Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”
Munthu Wodala
27 Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”
28 Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”
Chizindikiro cha Yona
29 Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona. 30 Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno. 31 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni. 32 Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.
Nyale ndi Thupi
33 “Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika. 34 Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima. 35 Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima. 36 Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”
Tsoka la Afarisi ndi Alembi Amalamulo
37 Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera. 38 Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja.
39 Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa. 40 Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja? 41 Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera.
42 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.
43 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika.
44 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”
45 Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?”
46 Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.
47 “Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha. 48 Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo. 49 Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’ 50 Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko, 51 kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.
52 “Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”
53 Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso, 54 pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.