Beginning
Fanizo la Wofesa Mbewu
4 Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. 2 Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: 3 “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4 Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5 Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6 Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8 Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”
9 Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
10 Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. 11 Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: 12 kotero kuti,
“ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu,
kumva mudzamva koma osamvetsetsa,
kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”
13 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? 14 Wofesa amafesa mawu. 15 Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. 16 Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. 17 Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. 18 Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; 19 koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. 20 Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”
Fanizo la Nyale
21 Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? 22 Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. 23 Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
24 Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. 25 Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”
Fanizo la Mbewu Imene Ikukula
26 Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. 27 Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. 28 Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. 29 Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
Fanizo la Mbewu ya Mpiru
30 Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? 31 Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. 32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
33 Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. 34 Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
Yesu Aletsa Namondwe
35 Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” 36 Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
40 Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”
Yesu Achiritsa Wogwidwa ndi Ziwanda
5 Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa. 2 Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. 3 Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo. 4 Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. 5 Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
6 Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake. 7 Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!” 8 Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”
9 Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?”
Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.” 10 Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
11 Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi. 12 Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, “Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo.” 13 Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
14 Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika. 15 Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha. 16 Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo. 17 Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.
18 Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo. 19 Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.” 20 Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.
Mtsikana Womwalira ndi Mayi Wodwala
21 Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja, 22 mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, 23 ndi kumudandaulira kwambiri nati, “Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo.” 24 Ndipo Yesu anapita naye.
Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye. 25 Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. 26 Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. 27 Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, 28 chifukwa anaganiza kuti, “Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa.” 29 Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
30 Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, “Ndani wakhudza zovala zanga?”
31 Ophunzira ake anayankha kuti, “Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ”
32 Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. 33 Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. 34 Anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako.”
35 Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”
36 Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”
37 Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo. 38 Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. 39 Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.” 40 Koma anamuseka Iye.
Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. 41 Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”) 42 Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri. 43 Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.