Beginning
Miyambo ya Makolo
15 Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti, 2 “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
3 Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu? 4 Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 5 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’ 6 iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu. 7 Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
8 “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
9 Amandilambira Ine kwachabe
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”
10 Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani. 11 Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
12 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
13 Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe. 14 Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
15 Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
16 Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? 17 Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi? 18 Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa. 19 Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe. 20 Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
Mayi wa ku Kanaani
21 Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. 22 Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
23 Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
24 Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”
25 Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”
26 Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”
27 Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”
28 Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
Yesu Adyetsa Anthu 4,000
29 Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi. 30 Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa. 31 Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
32 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”
33 Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”
34 Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”
35 Iye anawuza gululo kuti likhale pansi. 36 Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo. 37 Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri. 38 Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana. 39 Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.
Afarisi ndi Asaduki Afuna Chizindikiro
16 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.
2 Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira. 3 Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi. 4 Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.
Yisiti wa Afarisi ndi Asaduki
5 Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. 6 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”
7 Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.”
8 Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa. 9 Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? 10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? 11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.” 12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.
Petro Avomereza za Yesu
13 Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?”
14 Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”
15 Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?”
16 Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
17 Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba. 18 Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa. 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.” 20 Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.
22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.”
23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”
Za Kusenza Mtanda
24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. 25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.
28 “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”
Maonekedwe Aulemerero a Yesu pa Phiri
17 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. 2 Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. 3 Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.
4 Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
5 Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
6 Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. 7 Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” 8 Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.
9 Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
10 Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”
11 Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. 12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.” 13 Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.
Yesu Achiritsa Wodwala Matenda Akugwa
14 Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. 15 Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. 16 Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
17 Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.” 18 Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
19 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”
20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani. 21 Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”
Yesu Anena za Imfa yake Kachiwiri
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu. 23 Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.
Yesu Apereka Msonkho
24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”
Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”
26 Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”
Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.