Beginning
1 Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.
Mkazi wa Hoseya ndi Ana Ake
2 Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” 3 Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.
4 Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli. 5 Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”
6 Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. 7 Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”
8 Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna. 9 Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.
10 “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ 11 Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”
2 “Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”
Kulangidwa ndi Kubwezeretsedwa kwa Israeli
2 “Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo,
pakuti si mkazi wanga,
ndipo ine sindine mwamuna wake.
Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake,
ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
3 Akapanda kutero ndidzamuvula,
ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa;
ndidzamuwumitsa ngati chipululu,
adzakhala ngati dziko lopanda madzi,
ndi kumupha ndi ludzu.
4 Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake,
chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
5 Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere
ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi.
Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga,
zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,
ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
6 Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga;
ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
7 Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza;
adzazifunafuna koma sadzazipeza.
Pamenepo iye adzati,
‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja,
pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
8 Iye sanazindikire kuti ndine amene
ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta.
Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide,
zimene ankapangira mafano a Baala.
9 “Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola,
ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa.
Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa,
zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
10 Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake
pamaso pa zibwenzi zake;
palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
11 Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse:
zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano,
za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu,
imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake.
Ndidzayisandutsa chithukuluzi,
ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
13 Ndidzamulanga chifukwa cha masiku
amene anafukiza lubani kwa Abaala;
anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali
ndipo anathamangira zibwenzi zake,
koma Ine anandiyiwala,”
akutero Yehova.
14 “Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;
ndidzapita naye ku chipululu
ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15 Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,
ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.
Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,
monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
16 “Tsiku limeneli,” Yehova akuti,
“udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’
sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
17 Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake;
sadzatchulanso mayina awo popemphera.
18 Tsiku limenelo ndidzachita pangano
ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga.
Ndidzachotsa mʼdzikomo uta,
lupanga ndi zida zonse zankhondo,
kuti onse apumule mwamtendere.
19 Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya;
ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro,
mwachikondi ndi mwachifundo.
20 Ndidzakutomera mokhulupirika
ndipo udzadziwa Yehova.
21 “Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,”
akutero Yehova.
“Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo
ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
22 ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu,
vinyo ndi mafuta,
ndipo zidzamvera Yezireeli.
23 Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga:
ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’
Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’
ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”
Hoseya Ayanjana ndi Mkazi Wake
3 Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.”
2 Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. 3 Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.”
4 Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano. 5 Pambuyo pake Aisraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndi Davide mfumu yawo. Adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzalandira madalitso mʼmasiku awo otsiriza.
Yehova Ayimba Mlandu Israeli
4 Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova,
chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu
amene mumakhala mʼdzikoli:
“Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi
mulibe kulabadira za Mulungu.
2 Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha.
Kuba ndi kuchita chigololo;
machimo achita kunyanya
ndipo akungokhalira kuphana.
3 Chifukwa chake dziko likulira
ndipo onse amene amakhalamo akuvutika;
zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
4 “Koma wina asapeze mnzake chifukwa,
wina aliyense asayimbe mlandu mnzake,
pakuti anthu ako ali ngati anthu
amene amayimba mlandu wansembe.
5 Mumapunthwa usana ndi usiku
ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi.
Choncho ndidzawononga amayi anu.
6 Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.
“Pakuti mwakana kudziwa,
Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;
chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,
Inenso ndidzayiwala ana anu.
7 Ansembe ankati akachuluka
iwo ankandichimwiranso kwambiri;
iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
8 Amalemererapo pa machimo a anthu anga
ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
9 Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe.
Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo,
ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.
10 “Iwo azidzadya koma sadzakhuta;
azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana,
chifukwa anasiya Yehova
kuti adzipereke 11 ku zachiwerewere,
ku vinyo wakale ndi watsopano,
zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
12 za anthu anga.
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo
ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha.
Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa;
iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
13 Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri
ndi kufukiza lubani pa zitunda,
pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi,
pamene pali mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere
ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
14 “Ine sindidzalanga ana anu aakazi
pamene iwo adzachita zachiwerewere,
kapena akazi a ana anu
pamene adzachita zigololo.
Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,
ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako.
Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
15 “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli,
Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.
“Usapite ku Giligala.
Usapite ku Beti-Aveni.
Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
16 Aisraeli ndi nkhutukumve,
ngosamva ngati ana angʼombe.
Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji
ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
17 Efereimu waphathana ndi mafano;
mulekeni!
18 Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha,
amapitiriza kuchita zachiwerewere;
atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
19 Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu
ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.
Chiweruzo cha Israeli
5 “Ansembe inu, imvani izi!
Inu Aisraeli, tcherani khutu!
Inu nyumba yaufumu, mvetserani!
Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu:
Inu munali ngati msampha ku Mizipa,
munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
2 Owukira azama mʼmoyo wakupha,
Ine ndidzawalanga onsewo.
3 Ndimadziwa zonse za Efereimu;
Aisraeli ndi osabisika kwa Ine.
Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere;
Israeli wadziyipitsa.
4 “Ntchito zawo siziwalola
kubwerera kwa Mulungu wawo.
Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere;
Iwo sadziwa Yehova.
5 Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa;
Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo;
Yudanso anagwa nawo pamodzi.
6 Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo
kukapereka nsembe kwa Yehova,
iwo sadzamupeza;
Iye wawachokera.
7 Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova;
amabereka ana amʼchigololo
ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano
chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
8 “Womba lipenga mu Gibeya,
liza mbetete mu Rama.
Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni;
iwe Benjamini tsogolera.
9 Efereimu adzasanduka bwinja
pa tsiku la chilango.
Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi
pakati pa mafuko a Israeli.
10 Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu
amene amasuntha miyala ya mʼmalire.
Ndidzawakhutulira ukali wanga
ngati madzi a chigumula.
11 Efereimu waponderezedwa,
akulangidwa chifukwa chotsatira
mafano.
12 Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu,
ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
13 “Efereimu ataona nthenda yake,
ndi Yuda ataona zilonda zake,
pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya,
ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza.
Koma mfumuyo singathe kukuchizani,
singathe kuchiritsa mabala anu.
14 Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu.
Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda.
Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo;
ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
15 Ndipo ndidzabwerera ku malo anga
mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo.
Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga;
mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
Kusalapa kwa Israeli
6 “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Iye watikhadzula,
koma adzatichiritsa.
Iye wativulaza,
koma adzamanga mabala athu.
2 Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa;
pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa
kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3 Tiyeni timudziwe Yehova,
tiyeni tilimbike kumudziwa Iye.
Adzabwera kwa ife mosakayikira konse
ngati kutuluka kwa dzuwa;
adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe,
ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4 Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani?
Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda?
Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa,
ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5 Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga,
ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga;
chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6 Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe,
ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7 Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa,
iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8 Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa,
okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9 Monga momwe mbala zimadikirira anthu,
magulu a ansembe amachitanso motero;
iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu,
kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10 Ndaona chinthu choopsa kwambiri
mʼnyumba ya Israeli.
Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere,
ndipo Israeli wadzidetsa.
11 “Kunenanso za iwe Yuda,
udzakolola chilango.
“Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”
7 Pamene ndichiritsa Israeli,
machimo a Efereimu amaonekera poyera
ndiponso milandu ya Samariya sibisika.
Iwo amachita zachinyengo,
mbala zimathyola nyumba,
achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
2 Koma sazindikira kuti Ine
ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;
ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
3 “Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,
akalonga amasekerera mabodza awo.
4 Onsewa ndi anthu azigololo,
otentha ngati moto wa mu uvuni,
umene wophika buledi sasonkhezera
kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu
akalonga amaledzera ndi vinyo,
ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
6 Mitima yawo ili ngati uvuni;
amayandikira Mulungu mwachiwembu.
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,
mmawa umayaka ngati malawi a moto.
7 Onsewa ndi otentha ngati uvuni,
amapha olamulira awo.
Mafumu awo onse amagwa,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
8 “Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;
Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
9 Alendo atha mphamvu zake,
koma iye sakuzindikira.
Tsitsi lake layamba imvi
koma iye sakudziwa.
10 Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,
koma pa zonsezi
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake
kapena kumufunafuna.
11 “Efereimu ali ngati nkhunda
yopusa yopanda nzeru.
Amayitana Igupto
namapita ku Asiriya.
12 Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;
ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi
ndidzawakola.
13 Tsoka kwa iwo,
chifukwa andisiya Ine!
Chiwonongeko kwa iwo,
chifukwa andiwukira!
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa
koma amayankhula za Ine monama.
14 Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,
koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,
koma amandifulatira.
15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,
koma amandikonzera chiwembu.
16 Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;
ali ngati uta woonongeka.
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga
chifukwa cha mawu awo achipongwe.
Motero iwo adzasekedwa
mʼdziko la Igupto.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.