Beginning
1 Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.
2 Amosi anati:
“Yehova akubangula mu Ziyoni
ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu;
msipu wa abusa ukulira,
ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”
Chiweruzo pa Anthu Oyandikana ndi Israeli
3 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anapuntha Giliyadi
ndi zopunthira za mano achitsulo,
4 Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
5 Ndidzathyola chipata cha Damasiko;
ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni,
ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni.
Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,”
akutero Yehova.
6 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu
ndi kuwugulitsa ku Edomu,
7 ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
8 Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi
komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni.
Ndidzalanga Ekroni,
mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,”
akutero Ambuye Yehova.
9 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu,
osasunga pangano laubale lija,
10 Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”
11 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,
popanda nʼchifundo chomwe.
Popeza mkwiyo wake unakulabe
ndipo ukali wake sunatonthozeke,
12 Ine ndidzatumiza moto pa Temani
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”
13 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi
nʼcholinga choti akuze malire awo,
14 Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo,
kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
15 Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo,
iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,”
akutero Yehova.
2 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu,
mpaka kuwasandutsa phulusa,
2 Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu,
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti.
Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa,
mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.
3 Ndidzawononga wolamulira wake
ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,”
akutero Yehova.
4 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo akana lamulo la Yehova
ndipo sanasunge malangizo ake,
popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza,
milungu imene makolo awo ankayitsatira,
5 Ine ndidzatumiza moto pa Yuda,
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”
Chilango cha Anthu a ku Israeli
6 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva,
ndi osauka ndi nsapato.
7 Amapondereza anthu osauka
ngati akuponda fumbi,
ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa.
Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo,
ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
8 Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe
pa zovala zimene anatenga ngati chikole.
Mʼnyumba ya mulungu wawo
amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.
9 “Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo,
ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza
ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu.
Ndinawononga zipatso zawo
ndiponso mizu yawo.
10 “Ine ndinakutulutsani ku Igupto,
ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi,
kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri,
ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri.
Kodi si choncho, inu Aisraeli?”
akutero Yehova.
12 “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja,
ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.
13 “Tsono Ine ndidzakupsinjani
monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Munthu waliwiro sadzatha kuthawa,
munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga,
wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 Munthu wa uta sadzalimbika,
msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka,
ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri
adzathawa ali maliseche pa tsikulo,”
akutero Yehova.
Mboni Zotsutsa Israeli
3 Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:
2 “Inu nokha ndi amene ndinakusankhani
pakati pa mabanja onse a dziko lapansi;
nʼchifukwa chake ndidzakulangani
chifukwa cha machimo anu onse.”
3 Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi
asanapangane?
4 Kodi mkango umabangula mʼnkhalango
usanagwire nyama?
Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake
pamene sunagwire kanthu?
5 Kodi mbalame nʼkutera pa msampha
pamene palibe nyambo yake?
Kodi msampha umafwamphuka
usanakole kanthu?
6 Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda,
anthu sanjenjemera?
Pamene tsoka lafika mu mzinda,
kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?
7 Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu
asanawulule zimene akufuna kuchita
kwa atumiki ake, aneneri.
8 Mkango wabangula,
ndani amene sachita mantha?
Ambuye Yehova wayankhula,
ndani amene sanganenere?
9 Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi
ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:
“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;
onani chisokonezo pakati pake
ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
10 “Iwo sadziwa kuchita zolungama,
ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
11 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi:
“Mdani adzalizungulira dzikoli;
iye adzagwetsa malinga ako,
ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”
12 Yehova akuti,
“Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango
miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,
moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli
amene amakhala mu Samariya
pa msonga za mabedi awo,
ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
13 “Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,
ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;
nyanga za guwa zidzathyoka
ndipo zidzagwa pansi.
15 Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira
pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;
nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa
ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”
akutero Yehova.
Israeli Sanabwerere kwa Mulungu
4 Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya,
inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa
ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”
2 Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti,
“Nthawi idzafika ndithu
pamene adzakukokani ndi ngowe,
womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza.
3 Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma
aliyense payekhapayekha,
ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,”
akutero Yehova.
4 “Bwerani ku Beteli mudzachimwe;
ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa.
Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse,
bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.
5 Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko
ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu.
Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo,
pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,”
akutero Ambuye Yehova.
6 “Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse,
ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu.
Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”
akutero Yehova.
7 “Ndinenso amene ndinamanga mvula
patangotsala miyezi itatu kuti mukolole.
Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina,
koma pa mzinda wina ayi,
mvula inkagwa pa munda wina;
koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma.
8 Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi,
koma sanapeze madzi okwanira kumwa.
Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
akutero Yehova.
9 “Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa,
ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu.
Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi.
Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
akutero Yehova.
10 “Ine ndinabweretsa miliri pakati panu
monga ndinachitira ku Igupto.
Ndinapha anyamata anu ndi lupanga,
ndinapereka akavalo anu kwa adani.
Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo.
Komatu inu simunabwerere kwa Ine,”
akutero Yehova.
11 “Ndinawononga ena mwa inu
monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora.
Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto.
Komabe inu simunabwerere kwa Ine,”
akutero Yehova.
12 “Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli,
chifukwa ndidzakuchitira zimenezi,
konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.”
13 Iye amene amawumba mapiri,
amalenga mphepo,
ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake,
Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima,
ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi,
dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
Mawu Odandawulira Aisraeli
5 Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:
2 “Namwali Israeli wagwa,
moti sadzadzukanso,
wasiyidwa mʼdziko lake lomwe,
popanda woti ndi kumudzutsa.”
3 Ambuye Yehova akuti,
“Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu
udzatsala ndi anthu 100 okha;
mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu
udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
4 Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:
“Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;
5 musafunefune Beteli,
musapite ku Giligala,
musapite ku Beeriseba.
Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,
ndipo Beteli adzawonongekeratu.”
6 Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo,
mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto;
motowo udzawononga,
ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
7 Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa
ndi kunyoza chilungamo.
8 (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana,
amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa
ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku,
amene amayitana madzi a mʼnyanja
ndi kuwathira pa dziko lapansi,
Yehova ndiye dzina lake.
9 Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu
ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),
10 inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu
ndi kunyoza amene amanena zoona.
11 Mumapondereza munthu wosauka
ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu.
Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema,
inuyo simudzakhalamo.
Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa,
inu simudzamwa vinyo wake.
12 Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu
ndi kukula kwa machimo anu.
Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu
ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
13 Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu,
popeza ndi nthawi yoyipa.
14 Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa,
kuti mukhale ndi moyo.
Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu,
monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
15 Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino;
mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu.
Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo
anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.
16 Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena:
“Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula,
ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse.
Adzayitana alimi kuti adzalire,
ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
17 Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha,
pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,”
akutero Yehova.
Tsiku la Yehova
18 Tsoka kwa inu amene mumalakalaka
tsiku la Yehova!
Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova?
Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.
19 Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango
amakumana ndi chimbalangondo,
ngati pamene munthu walowa mʼnyumba,
natsamira dzanja lake pa khoma
ndipo njoka nʼkuluma.
20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala,
mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?
21 “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza;
sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya,
Ine sindidzazilandira.
Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano,
Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 Musandisokose nazo nyimbo zanu!
Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi,
chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
25 “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja
munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?
26 Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu,
ndi nyenyezi ija Kaiwani,
mulungu wanu,
mafano amene munadzipangira.
27 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,”
akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.