Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 16-17

Kusakhulupirika kwa Yerusalemu

16 Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Yerusalemu za ntchito zake zonyansa. Umuwuze kuti, ‘Ambuye Yehova akukuwuza, iwe Yerusalemu kuti: Kwawo kwa makolo ako ndi ku Kanaani ndipo iwe unabadwira komweko. Abambo ako anali Mwamori, amayi ako anali Mhiti. Pa tsiku lomwe unabadwa sanadule mchombo wako. Sanakusambitse mʼmadzi kuti uyere. Sanakuthire mchere kapena kukukulunga mʼnsalu. Palibe ndi mmodzi yemwe anakusamala kapena kukumvera chisoni kuti akuchitire zimenezi. Mʼmalo mwake anakutaya panja poyera, chifukwa ananyansidwa nawe pa tsiku lako lobadwa.

“ ‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’ ndi kuti ukule ngati mbewu ya mʼmunda. Iwe unakula ndipo unatalika ndi kutha msinkhu. Mawere ako anayamba kumera ndi tsitsi lakonso linayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiwa.

“ ‘Tsono pamene ndinkadutsanso ndinaona kuti nthawi yako yomanga banja inakwana. Tsono ndinakufunditsa chovala changa ndi kubisa umaliseche wako. Ndinachita nawe pangano la ukwati ndipo unakhala wanga, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.

“ ‘Ine ndinakusambitsa mʼmadzi kutsuka magazi ako ndikukudzoza mafuta. 10 Ndinakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato za chikopa. Ndinakuveka zovala zabafuta ndi kukuveka zovala za bafuta. 11 Ndinakukongoletsa ndi zokometsera zamtengowapatali: ndinakuveka zibangiri mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako, 12 ndipo ndinakuveka chipini pa mphuno yako, ndolo ku makutu ako ndiponso chipewa chaufumu pa mutu wako. 13 Choncho unavala zokongoletsa zagolide ndi siliva. Zovala zako zinali zabafuta, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Chakudya chako chinali ufa wosalala uchi ndi mafuta a olivi. Motero unakhala wokongola kwambiri ndipo unasanduka mfumukazi. 14 Ndipo mbiri ya kukongola kwako inawanda pakati pa anthu a mitundu ina, chifukwa ulemerero umene ndinakupatsa unapititsa patsogolo kukongola kwako, akutero Ambuye Yehova.

15 “ ‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake. 16 Unatenga zovala zako zina nukakongoletsera malo opembedzerako mafano, ndipo kumeneko umachitirako zigololo. Zinthu izi sizinachitikepo nʼkale lomwe ndipo sizidzachitikanso. 17 Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama. 18 Ndipo iwe unatenga zovala zako zopetapeta ndi kuveka mafano. Mafuta anga ndi lubani wanga unapereka kwa mafanowo. 19 Chakudya chimene ndinakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi, zimene ndinkakudyetsa nazo unazitenga nʼkuzipereka kwa mafanowo ngati nsembe ya fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

20 “ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire 21 kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? 22 Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.

23 “ ‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse, 24 wadzimangira wekha nsanja ndi guwa pa mabwalo onse. 25 Pa msewu uliwonse wamanga nsanjazo. Motero wanyazitsa kukongola kwako podzipereka kwa aliyense amene adutsapo. 26 Umachita chigololo ndi Aigupto, anthu adama oyandikana nawe. Choncho unandikwiyitsa chifukwa unachulukitsa za dama zako. 27 Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa. 28 Chifukwa cha chilakolako chako unachitanso zadama ndi Aasiriya. Ngakhale unachita nawo chigololo koma sunakhutitsidwebe. 29 Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.

30 “ ‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi. 31 Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro.

32 “ ‘Iwe mkazi wachigololo! Umakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wakowako! 33 Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. 34 Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.

35 “ ‘Tsono mkazi wachigololo iwe, imva mawu a Yehova! 36 Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano, 37 nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse. 38 Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri. 39 Ndidzakupereka mʼmanja mwa zibwenzi zako ndi kuwononga nyumba zopembedzera mafano ako. Iwo adzakuvula zovala zako ndi kutenga zodzikometsera zako zabwino. Choncho adzakusiya wa maliseche ndi wausiwa. 40 Iwo adzabweretsa gulu la anthu limene lidzakuponya miyala ndi kukutematema ndi malupanga awo. 41 Adzatentha nyumba zako ndi kukulanga iwe pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa chigololo chako, ndipo sudzalipiranso zibwenzi zako. 42 Ukali wanga udzalekera pamenepo ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala chete osakwiyanso.

43 “ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.

44 “ ‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’ 45 Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori. 46 Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi. 47 Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo. 48 Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ngakhale mʼbale wako Sodomu ndi ana ake aakazi sanachitepo zimene iwe ndi ana ako aakazi munachita.

49 “ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. 50 Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu. 51 Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye. 52 Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.

53 “ ‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu. 54 Ndidzatero kuti uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa cha zonse zimene unachita powatonthoza anthuwa. 55 Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja. 56 Kale lija pamene unkanyada, suja unkanyogodola mʼbale wako Sodomu 57 kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza. 58 Choncho udzalangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi machitidwe anu onyansa, akutero Yehova.

59 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulanga molingana ndi zimene unachita. Iwe unanyoza lumbiro lako pophwanya pangano langa. 60 Komabe, Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinachita nawe mʼmasiku a unyamata wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha ndi iwe. 61 Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe. 62 Kotero ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 63 Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Fanizo la Ziwombankhanga Ziwiri ndi Mtengo Wamphesa

17 Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, aphere mwambi anthu a Israeli ndi kuwawuza fanizo. Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza. Chinabudula msonga yeniyeni ya nthambiyo nʼkupita nayo ku dziko lamalonda ndipo anakayika mu mzinda wa anthu amalonda.

“ ‘Kenaka chinatenga mbewu ina ya mʼdziko ndi kukayidzala ku malo a chonde kumene kunali madzi ambiri. Anayidzala ngati mmene amadzalira mtengo wa msondozi. Ndipo inaphuka nisanduka mtengo wa mpesa wotambalala chamʼmunsi. Nthambi zake zinaloza mmwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake inalowa pansi. Kotero unakhala mtengo wamphesa ndipo unasanduka wa nthambi ndiponso wa masamba ambiri.

“ ‘Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu, cha mapiko amphamvu ndi cha nthenga zambiri. Tsopano mtengo wamphesa uja unakhotetsera mizu yake kwa chiwombankhangacho kuchokera pa malo amene unadzalidwa ndipo unatambalitsa nthambi zake kwa chiwombankhangacho kufuna kuthiridwa madzi. Koma mtengowo unadzalidwa kale pa nthaka yabwino mʼmbali mwa madzi kuti ukhale ndi nthambi zambiri, ubereke zipatso ndi kukhala wokongola.’

“Ukawawuze Aisraeli kuti, ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Kodi udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzawuzula mizu ndi kubudula nthambi zake kuti ufote? Masamba ake onse anthete adzafota. Sipadzafunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti awuzule. 10 Ngakhale utawokedwa pena, kodi udzaphuka? Kodi sudzafoteratu mphepo ya kummawa ikadzawomba, kufotera pa malo pamene anawuwokerapo?’ ”

11 Kenaka Yehova anandiyankhula nati: 12 “Tawafunsa anthu owukirawa kuti, ‘kodi mukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Uwafotokozere kuti, ‘Mfumu ya Babuloni inapita ku Yerusalemu ndikukatengako mfumu ndi anthu ake otchuka ndi kubwera nawo ku Babuloni. 13 Ndipo anatenga mmodzi wa banja laufumu ndi kuchita naye mgwirizano, ndipo anamulumbiritsa kuti akhale womvera. Inatenganso akulu onse a mʼdzikomo 14 kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzaphukenso, koma kuti ukhalepobe posunga pangano limene unachita. 15 Koma mfumu inawukira mfumu ya ku Babuloni potumiza nthumwi ku dziko la Igupto kukatenga akavalo ndi gulu lalikulu la nkhondo. Kodi mfumu yotereyi ingapambane? Kodi wochita zinthu zoterezi angapulumuke? Kodi angaphwanye mgwirizano ndi kupulumuka?

16 “ ‘Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, mfumuyo idzafera ku Babuloni, mʼdziko la mfumu imene inayika pa mpando waufumu. Inapeputsa lumbiro lake nʼkuphwanya pangano limene inachita ndi mfumu inayo. 17 Farao ndi gulu lake lankhondo lamphamvu sadzatha kumuthandiza pa nkhondo, pamene mfumu ya Babuloni idzapanga mitumbira ya nkhondo ndi nsanja za nkhondo kuti iwononge miyoyo yambiri. 18 Mfumu ya ku Yuda inanyoza lumbiro lake pophwanya pangano. Inalonjeza komabe sinatsatire malonjezo ake. Choncho sidzapulumuka.

19 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndithu pali Ine wamoyo, Ine ndidzalanga mfumu imeneyi chifukwa inanyoza lumbiro langa, ndi kuphwanya pangano langa. 20 Ndidzayitchera ukonde ndipo idzakodwa mu msampha wanga. Ndidzapita nayo ku Babuloni ndi kuyilanga kumeneko chifukwa inali yosakhulupirika kwa Ine. 21 Asilikali ake onse amene akuthawa adzaphedwa ndi lupanga, ndipo opulumuka adzabalalitsidwa ku mbali zonse. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova ndayankhula.

22 “ ‘Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndidzatenga nthambi pamwamba penipeni pa mkungudza ndi kuyidzala; ndidzathyola nthambi yanthete kuchokera pa nthambi zapamwamba penipeni ndi kuyidzala pamwamba pa phiri lalitali. 23 Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake. 24 Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma.

“ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.