Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
117 Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
2 Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.
Tamandani Yehova.
31 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
2 Yehova akuti,
“Anthu amene anapulumuka ku nkhondo
ndinawakomera mtima mʼchipululu;
pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”
3 Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,
“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.
Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
4 Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;
mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,
ndipo mudzapita kukavina nawo
anthu ovina mwachimwemwe.
5 Mudzalimanso minda ya mpesa
pa mapiri a Samariya;
alimi adzadzala mphesa
ndipo adzadya zipatso zake.
6 Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula
pa mapiri a Efereimu nati,
‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,
kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”
Mawu Oyamba
1 Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu, 2 monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. 3 Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, 4 kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.