Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 142

Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.

142 Ndikulirira Yehova mofuwula;
    ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;
    ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,
    ndinu amene mudziwa njira yanga.
Mʼnjira imene ndimayendamo
    anthu anditchera msampha mobisa.
Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;
    palibe amene akukhudzika nane.
Ndilibe pothawira;
    palibe amene amasamala za moyo wanga.

Ndilirira Inu Yehova;
    ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,
    gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
Mverani kulira kwanga
    pakuti ndathedwa nzeru;
pulumutseni kwa amene akundithamangitsa
    pakuti ndi amphamvu kuposa ine.
Tulutseni mʼndende yanga
    kuti nditamande dzina lanu.

Ndipo anthu olungama adzandizungulira
    chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Habakuku 3:1-16

Pemphero la Habakuku

Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.

Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;
    Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.
Muzichitenso masiku athu ano,
    masiku athu ano zidziwike;
    mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,
    Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.
            Sela
Ulemerero wake unaphimba mlengalenga
    ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;
    kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,
    mʼmene anabisamo mphamvu zake.
Patsogolo pake pankagwa mliri;
    nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.
Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;
    anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.
Mapiri okhazikika anagumuka
    ndipo zitunda zakalekale zinatitimira.
    Njira zake ndi zachikhalire.
Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,
    mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?
    Kodi munakalipira timitsinje?
Kodi munapsera mtima nyanja
    pamene munakwera pa akavalo anu
    ndiponso magaleta anu achipulumutso?
Munasolola uta wanu mʼchimake,
    munayitanitsa mivi yambiri.
            Sela
Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;
10     mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.
Madzi amphamvu anasefukira;
    nyanja yozama inakokoma
    ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.

11 Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,
    pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,
    pa kunyezimira kwa mkondo wanu.
12 Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,
    ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.
13 Munapita kukalanditsa anthu anu,
    kukapulumutsa wodzozedwa wanu.
Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,
    munawononga anthu ake onse.
            Sela
14 Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake
    pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa,
ankasangalala ngati kuti akudzawononga
    osauka amene akubisala.
15 Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,
    kuvundula madzi amphamvu.

16 Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri,
    milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo;
mafupa anga anaguluka,
    ndipo mawondo anga anawombana.
Komabe ndikuyembekezera mofatsa,
    tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.

Yuda 5-21

Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire. Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha.

Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba. Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!” 10 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ndipo zinthu zimene amazidziwa ndi nzeru zachibadwa, monga za nyama, ndizo zimene zimawawononga.

11 Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.

12 Anthu amenewa ndiwo amayipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mopanda manyazi ndipo ali ngati abusa amene amangodzidyetsa okha. Anthuwa ali ngati mitambo yowuluzika ndi mphepo, yopanda mvula. Ali ngati mitengo ya nthawi ya masika, yopanda zipatso, yozuka mizu, mitengo yoferatu. 13 Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.

14 Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira pa Adamu, ananeneratu za anthu amenewa kuti, “Onani, Ambuye akubwera ndi oyera ake osawerengeka 15 kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.” 16 Anthu amenewa amangʼungʼudza ndi kudandaula. Amatsatira zilakolako zawo zoyipa. Amayankhula zodzitamandira ndipo amanamiza ena pofuna kupeza phindu.

Awalimbikitsa kuti Apirire

17 Koma okondedwa, kumbukirani zimene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu ananeneratu. 18 Iwo anakuwuzani kuti, “Mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsatira zofuna zawo zoyipa.” 19 Anthu amenewa ndi amene akubweretsa mipatuko pakati panu, amatsatira nzeru zachibadwa ndipo alibe Mzimu Woyera.

20 Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. 21 Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.