Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Luka 1:68-79

68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli
    chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife
    mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),
71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu
    ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu
    ndi kukumbukira pangano lake loyera,
73     lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,
    ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
75     mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.

76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;
    pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso
    kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,
    ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
79 kuwalira iwo okhala mu mdima
    ndi mu mthunzi wa imfa,
kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”

Yeremiya 21

Mulungu Akana Pempho la Zedekiya

21 Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya. Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”

Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali. Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa. Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’

“Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. 10 Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.

11 “Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova; 12 inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti,

“ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse;
    pulumutsani mʼdzanja la wozunza
    aliyense amene walandidwa katundu wake,
kuopa kuti ukali wanga ungabuke
    ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika
    chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.
13 Ndidzalimbana nanu,
    inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa,
    inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,
            akutero Yehova.
Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe?
    Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’
14 Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu,
            akutero Yehova.
Ndidzatentha nkhalango zanu;
    moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’ ”

Ahebri 9:23-28

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. 25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake. 26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. 27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, 28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.