Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 142

Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.

142 Ndikulirira Yehova mofuwula;
    ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;
    ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,
    ndinu amene mudziwa njira yanga.
Mʼnjira imene ndimayendamo
    anthu anditchera msampha mobisa.
Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;
    palibe amene akukhudzika nane.
Ndilibe pothawira;
    palibe amene amasamala za moyo wanga.

Ndilirira Inu Yehova;
    ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,
    gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
Mverani kulira kwanga
    pakuti ndathedwa nzeru;
pulumutseni kwa amene akundithamangitsa
    pakuti ndi amphamvu kuposa ine.
Tulutseni mʼndende yanga
    kuti nditamande dzina lanu.

Ndipo anthu olungama adzandizungulira
    chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Habakuku 3:17-19

17 Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,
    ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.
Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,
    ndipo mʼminda musatuluke kanthu.
Ngakhale nkhosa
    ndi ngʼombe zithe mʼkhola,
18 komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,
    ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

19 Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;
    amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,
    amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.

Luka 19:11-27

Antchito Opindula Mosiyana

11 Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. 12 Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. 13 Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’

14 “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’

15 “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.

16 “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’

17 “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’

18 “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’

19 “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’

20 “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. 21 Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’

22 “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? 23 Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’

24 “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”

25 Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”

26 Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 27 Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.