Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 145:1-5

Salimo la matamando la Davide.

145 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;
    ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku
    ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;
    ukulu wake palibe angawumvetsetse.
Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;
    Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,
    ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

Masalimo 145:17-21

17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,
    ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,
    onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
19 Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;
    amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
20 Yehova amayangʼana onse amene amamukonda
    koma adzawononga anthu onse oyipa.

21 Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.
    Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera
    ku nthawi za nthawi.

Zekariya 1:1-17

Yuda Abwerera kwa Yehova

Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:

“Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova. Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu?

“Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ”

Munthu Pakati pa Mitengo ya Mchisu

Tsiku la 24 la mwezi wa 11, mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.

Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera.

Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?”

Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.”

10 Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.”

11 Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.”

12 Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?” 13 Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane.

14 Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, “Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni, 15 koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.’

16 “Choncho, Yehova akuti, ‘Ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo, nyumba yanga adzayimanganso kumeneko. Ndipo adzatenganso chingwe choyezera kuti amange Yerusalemu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

17 “Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ”

Machitidwe a Atumwi 22:22-23:11

Paulo Nzika ya Chiroma

22 Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”

23 Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba, 24 mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere. 25 Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”

26 Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”

27 Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?”

Paulo anayankha kuti, “Inde.”

28 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.”

Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”

29 Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.

Paulo ku Bwalo Lalikulu la Ayuda

30 Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.

23 Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.” Chifukwa cha mawu amenewa, mkulu wa ansembe Ananiya analamulira amene anali pafupi ndi Paulo kuti amumenye pakamwa. Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”

Anthu amene anayimirira pafupi ndi Paulo anati, “Bwanji ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?”

Paulo anayankha nati, “Abale, ine sindinazindikire kuti ndi mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa kuti, ‘Usayankhule zoyipa kwa mtsogoleri wa anthu ako.’ ”

Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.” Iye atanena zimenezi, mkangano unabuka pakati pa Afarisi ndi Asaduki mpaka anthu kugawikana. Asaduki amati kulibe kuuka kwa akufa, kulibenso ngakhale angelo kapena mizimu, koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.

Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.” 10 Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.

11 Usiku omwewo Ambuye anayimirira pambali pa Paulo nati, “Limba mtima! Monga wandichitira Ine umboni mu Yerusalemu, moteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.