Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 76

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu.

76 Mulungu amadziwika mu Yuda;
    dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
Tenti yake ili mu Salemu,
    malo ake okhalamo mu Ziyoni.
Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka,
    zishango ndi malupanga, zida zankhondo.
            Sela

Wolemekezeka ndinu,
    wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma,
    Iwowo amagona tulo tawo totsiriza;
palibe mmodzi wamphamvu
    amene angatukule manja ake.
Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo,
    kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa.
    Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo,
    ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze,
    kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko.
            Sela
10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando
    ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.

11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse;
    anthu onse omuzungulira abweretse mphatso
    kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
12 Iye amaswa mzimu wa olamulira;
    amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.

Yesaya 60:17-22

17 Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa,
    ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo.
Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa
    ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala.
Olamulira ako adzakhala a mtendere.
    Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
18 Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako,
    bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako,
ndidzakhala malinga ako okuteteza
    ndipo udzanditamanda.
19 Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire,
    kapena mwezi kuti uwunikire usiku,
pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya,
    ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20 Dzuwa lako silidzalowanso,
    ndipo mwezi wako sudzazimiriranso;
Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya,
    ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
21 Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama
    ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya.
Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala,
    ntchito ya manja anga,
    kuti aonetse ulemerero wanga.
22 Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko,
    kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu.
Ine ndine Yehova,
    nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”

Aefeso 4:25-5:2

25 Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. 26 Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. 27 Musamupatse mpata Satana. 28 Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.

29 Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. 30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. 31 Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. 32 Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.

Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.